Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 8

N’chifukwa Chiyani Timavala Bwino Tikamapita Kumisonkhano Yathu?

N’chifukwa Chiyani Timavala Bwino Tikamapita Kumisonkhano Yathu?

Iceland

Mexico

Guinea-Bissau

Philippines

Kodi mwaona m’zithunzi zomwe zili m’kabuku kano kuti anthu a Mboni za Yehova amavala bwino kwambiri akamapita kumisonkhano yawo yampingo? N’chifukwa chiyani timayesetsa kuvala bwino komanso kuoneka bwino pamisonkhano?

Timachita zimenezi posonyeza ulemu kwa Mulungu wathu. N’zoona kuti Mulungu samangoona mmene tikuonekera kunja, koma amaonanso mumtima mwathu. (1 Samueli 16:7) Komabe tikasonkhana kuti timulambire, timafunitsitsa kusonyeza ulemu kwa iyeyo komanso kwa Akhristu anzathu. Mwachitsanzo, ngati tikukaonekera pamaso pa woweruza kukhoti, tingayesetse kuvala bwino komanso kuoneka bwino. Tingachite zimenezi posonyeza kulemekeza woweruzayo. Chimodzimodzinso ifeyo. Mmene tavalira popita kumisonkhano yathu zimasonyeza kuti tikulemekeza “Woweruza wa dziko lonse lapansi,” yemwe ndi Yehova Mulungu. Komanso timasonyeza kuti tikulemekeza malo amene tikumulambirirawo.—Genesis 18:25.

Timachita zimenezi posonyeza kuti tikutsatira mfundo zimene timaphunzira. Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti azivala “mwaulemu ndi mwanzeru.” (1 Timoteyo 2:9, 10) Kuvala “mwaulemu” kukutanthauza kupewa zovala zomwe zingasonyeze kuti tikudzionetsera ndiponso zosonyeza kusadzilemekeza. Komanso kuchita zinthu “mwanzeru” kumatithandiza kupewa kuvala motayirira, monga kuvala zovala zothina, zazifupi, kapenanso zazikulu kwambiri. Ngakhale kuti timatsatira mfundo za m’Baibulo zimenezi, timakhalabe ndi mwayi wosankha zovala zimene tikufuna. Mavalidwe ndi maonekedwe athu ‘angakometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu ndiponso angatamande Mulungu,’ ngakhale pamene sitinalankhule chilichonse. (Tito 2:10; 1 Petulo 2:12) Choncho, tikavala bwino popita kumisonkhano, timathandiza kuti ena aziona kulambira Yehova m’njira yoyenera.

Musalephere kupita ku Nyumba ya Ufumu poganiza kuti zovala zanu si zabwino. Chimene chimafunika ndi zovala zochapa bwino komanso zoyenerera, osati zatsopano kapena zamtengo wapatali zokhazokha.

  • Kodi kuvala bwino polambira Mulungu n’kofunika motani?

  • Posankha zochita pa nkhani ya kavalidwe ndi kaonekedwe kathu, kodi ndi mfundo ziti zimene zingatithandize?