Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 23

Kodi Ntchito Yolemba Ndiponso Kumasulira Mabuku Athu Imayenda Bwanji?

Kodi Ntchito Yolemba Ndiponso Kumasulira Mabuku Athu Imayenda Bwanji?

Dipatimenti Yolemba, m’dziko la United States

South Korea

Armenia

Burundi

Sri Lanka

Kuti ntchito yathu yolengeza “uthenga wabwino . . . kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse” iziyenda bwino, timasindikiza mabuku m’zinenero zoposa 750. (Chivumbulutso 14:6) Kodi timakwanitsa bwanji ntchito yovutayi? Ntchitoyi imatheka chifukwa imagwiridwa ndi anthu olemba nkhani ochokera m’mayiko osiyanasiyana komanso anthu omasulira omwe amagwira ntchito yawo modzipereka, ndipo onsewa ndi a Mboni za Yehova.

Nkhani zonse zimalembedwa m’Chingelezi. Bungwe Lolamulira limayang’anira ntchito za Dipatimenti Yolemba imene ili ku likulu lathu la padziko lonse. Dipatimenti imeneyi imayang’anira ntchito ya anthu olemba nkhani amene akutumikira kulikulu lathu komanso m’maofesi ena a Mboni za Yehova. Popeza kuti amene amalemba nkhani zathu akuchokera m’mayiko osiyanasiyana, zimenezi zimathandiza kuti nkhanizo zikhale zokhudza anthu a m’mayiko ambiri komanso azikhalidwe zosiyanasiyana.

Kenako nkhanizo zimatumizidwa kwa omasulira. Nkhani zikalembedwa zimaonedwa ndi anthu osiyanasiyana amene amatsimikizira kuti zili bwino. Kenako amazitumiza kwa omasulira padziko lonse, amene amagwira ntchito m’magulu. Omasulirawa amayesetsa kusankha “mawu olondola a choonadi” amene ali ndi tanthauzo lenileni la mawu a Chingelezi omwe akuwamasulirawo.​—Mlaliki 12:10.

Makompyuta amathandiza kuti ntchitoyi iziyenda mwamsanga. N’zoona kuti kompyuta payokha singagwire ntchito imene olemba nkhani komanso omasulirawa amagwira. Komabe, kuti azigwira ntchitoyi mofulumira kwambiri iwo amagwiritsa ntchito madikishonale ndi mapulogalamu ena apakompyuta. A Mboni za Yehova ali ndi pulogalamu yawo ya pakompyuta [Multilanguage Electronic Publishing System (MEPS)] yomwe amagwiritsa ntchito pokonza mabuku m’zinenero zambirimbiri. Pulogalamu imeneyi imathandiza poika zithunzi ndi kukonza mmene mabuku adzaonekere akadzasindikizidwa.

N’chifukwa chiyani timachita zonsezi, ngakhale m’zinenero zimene zimalankhulidwa ndi anthu ochepa kwambiri? N’chifukwa chakuti Yehova akufuna kuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.”​—1 Timoteyo 2:3, 4.

  • Kodi ntchito yolemba mabuku athu imayenda bwanji?

  • N’chifukwa chiyani timamasulira mabuku athu m’zinenero zambiri?