Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 10

Kodi Kulambira kwa Pabanja N’chiyani?

Kodi Kulambira kwa Pabanja N’chiyani?

South Korea

Brazil

Australia

Guinea

Kuyambira kale, Yehova wakhala akufuna kuti mabanja azikhala ndi nthawi yochitira zinthu pamodzi n’cholinga choti alimbitse ubwenzi wawo ndi iye komanso kuti banja lawo lilimbe. (Deuteronomo 6:6, 7) N’chifukwa chake banja lililonse la Mboni za Yehova linasankha nthawi imene limachita kulambira kwa pabanja mlungu uliwonse. Pa nthawiyi, banja limakambirana momasuka zinthu zauzimu zogwirizana kwambiri ndi banja lawo. Ngati mukukhala nokha, nthawi imeneyi mungaigwiritse ntchito kuti muyandikire Mulungu. Mungachite zimenezi pophunzira Baibulo pa nkhani imene mungasankhe.

Imakhala nthawi yoyandikira kwambiri Yehova. Baibulo limati: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” ( Yakobo 4:8) Kuphunzira Mawu a Mulungu kumatithandiza kuti timudziwe bwino Yehova. Timadziwa bwino makhalidwe ake komanso mmene iye amachitira zinthu. Njira yosavuta yoyambira kulambira kwa pabanja ndi kuyamba ndi kuwerenga limodzi Baibulo mokweza mwina pogwiritsa ntchito ndandanda yowerenga Baibulo ya mlungu umenewo ya msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Munthu aliyense m’banjamo angapatsidwe ndime zina m’Baibulo zoti awerenge kenako onse n’kukambirana mfundo zimene aphunzira pa zimene awerengazo.

Imakhala nthawi yabwino yoti onse m’banjamo alimbitse ubwenzi wawo. Banja likamaphunzirira limodzi Baibulo, zimathandiza kuti mwamuna ndi mkazi wake azikondana komanso kuti ana azikondana ndi makolo awo. Nthawi yophunzirayo iyenera kukhala nthawi yosangalatsa kwambiri imene aliyense angaiyembekezere mwachidwi mlungu uliwonse. Makolo angasankhe nkhani zimene angaphunzire, mogwirizana ndi msinkhu wa ana awo, mwina pogwiritsa ntchito nkhani za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kapena pawebusaiti yathu ya jw.org. Mwina mungakambirane za vuto linalake limene ana anu akumana nalo kusukulu ndi zimene anawo angachite kuti athane nalo. Mukhozanso kuonera pulogalamu iliyonse pa TV ya JW Broadcasting (tv.jw.org/ny) n’kukambirana zimene mwaonerazo. Mungasangalalenso kukonzekera nyimbo zomwe zidzaimbidwe kumisonkhano kenako n’kudya tizakudya ndi tizakumwa pambuyo pa kulambirako.

Nthawi yapadera imeneyi, yomwe banja lanu lizilambira Yehova limodzi mlungu uliwonse, idzathandiza kuti aliyense m’banja lanu azisangalala ndi Mawu a Mulungu, ndipo Yehova adzadalitsa kwambiri khama lanu.​—Salimo 1:1-3.

  • N’chifukwa chiyani timapatula nthawi yoti tizichita Kulambira kwa Pabanja?

  • Kodi makolo angachite chiyani kuti nthawi imeneyi izikhala yosangalatsa kwa aliyense m’banjamo?