Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 9

Kodi Tingatani Kuti Tizikonzekera Bwino Misonkhano?

Kodi Tingatani Kuti Tizikonzekera Bwino Misonkhano?

Cambodia

Ukraine

Ngati mukuphunzira Baibulo ndi wa Mboni za Yehova, muyenera kuti nthawi zonse mumayesetsa kukonzekera zimene muphunzirezo. Kuti muzipindula kwambiri ndi misonkhano ya mpingo, ndi bwino kukonzekeranso musanapite kumisonkhanoko. Zinthu zingakuyendereni bwino ngati mutakhala ndi ndandanda yabwino yokuthandizani kukonzekera.

Sankhani nthawi ndiponso malo abwino ophunzirira. Kodi ndi nthawi iti imene mungakonzekere bwino popanda chododometsa? Kodi ndi m’mawa kwambiri musanayambe kugwira ntchito, kapena usiku ana onse atagona? Ngakhale mutamaphunzira kwa nthawi yochepa, patulani nthawi imene mukufuna kuti muziphunzirayo, ndipo musalole chilichonse kukudodometsani kapena kukulepheretsani kuphunzira. Sankhani malo opanda phokoso, ndipo muonetsetse kuti palibe chilichonse chimene chingakusokonezeni. Mungachite zimenezi pothimitsa TV, foni ndiponso wailesi. Kupemphera musanayambe kuphunzira kungakuthandizeni kuti musakhale ndi nkhawa chifukwa cha zinthu za tsikulo, ndipo zimenezi n’zofunika kuti maganizo anu onse akhale pa Mawu a Mulungu amene mukufuna kuphunzirawo.​—Afilipi 4:6, 7.

Muzidula mzere kunsi kwa mfundo zimene mwapeza, pokonzekera kuti mukayankhe. Mukamayamba kukonzekera, muziona kaye nkhani yonse mwachidule kuti mukhale ndi chithunzi cha nkhaniyo. Mungachite zimenezi poganizira mutu wa nkhaniyo, komanso mmene timitu tamkati tikugwirizanira ndi mutu waukulu. Muzionanso zithunzi ndiponso mafunso obwereza amene akusonyeza mfundo zikuluzikulu za nkhaniyo. Mukatero, werengani ndime iliyonse ndi funso lake n’kuyesetsa kupeza yankho la funsolo. Muziwerenga m’Baibulo lanu malemba amene ali m’nkhaniyo n’kuganizira mmene akugwirizanira ndi nkhani yonseyo. (Machitidwe 17:11) Mukapeza yankho la funso la ndime imeneyo, dulani mzere kunsi kwa mfundo zofunika payankho limenelo, zimene zingakuthandizeni kuti mudzalikumbukire. Ndiyeno mukapita kumisonkhano, mungakweze dzanja kuti muyankhe mwachidule m’mawu anuanu.

Mukamakonzekera nkhani zosiyanasiyana zimene timaphunzira mlungu uliwonse kumisonkhano, mudzawonjezera mfundo zatsopano za m’Baibulo mumtima wanu, womwe uli ngati ‘chosungiramo chuma.’​—Mateyu 13:51, 52.

  • Kodi mungatsatire ndandanda yotani pokonzekera misonkhano?

  • Kodi mungakonzekere bwanji kuti mukapereke ndemanga pamisonkhano?