Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 26

Kodi Tingathandize Bwanji Kuti Nyumba Yathu ya Ufumu Izioneka Bwino?

Kodi Tingathandize Bwanji Kuti Nyumba Yathu ya Ufumu Izioneka Bwino?

Estonia

Zimbabwe

Mongolia

Puerto Rico

Nyumba ya Ufumu iliyonse ya Mboni za Yehova imadziwika ndi dzina loyera la Mulungu. Choncho timaona kuti kuisamalira kuti izioneka bwino, ndiponso kukonza zinthu zomwe zawonongeka mkati ndi kunja, ndi mwayi waukulu komanso ndi mbali ya kulambira kwathu. Ndipo aliyense ali ndi mwayi wochita nawo zimenezi.

Muzikonza nawo m’Nyumba ya Ufumu misonkhano ikatha. Pambuyo pa msonkhano uliwonse, abale ndi alongo amaonetsetsa kuti asanachoke, asesa m’Nyumba ya Ufumu. Komanso kamodzi pa mlungu, mpingo umafunika kukonza bwino Nyumba ya Ufumu. Mkulu kapena mtumiki wothandiza ndi amene amayang’anira ntchito imeneyi ndipo nthawi zambiri amakhala ndi ndandanda ya ntchito zomwe zikufunika kugwiridwa. Mogwirizana ndi zofunika kumpingo kwawo, abale ndi alongo angadzipereke kusesa, kukolopa, kupukuta mipando, kukonza kuzimbudzi, kutsuka mawindo, kutaya zinyalala kapena kusamalira zinthu zina kunja kwa Nyumba ya Ufumuyo. Ndipo nthawi zina kamodzi pachaka, mpingo umakonza zoti pakhale ntchito yaikulu yokonza zinthu. Tiyenera kutenganso ana athu kuti akagwire nawo ntchito ngati zimenezi. Tikamachita zimenezi timathandiza anawo kuti azilemekeza malo athu olambirira.​—Mlaliki 5:1.

Muzithandiza nawo pokonza zinthu zowonongeka. Chaka chilichonse, mpingo uliwonse umafufuza zinthu zimene zikufunika kukonzedwa mkati ndi kunja kwa Nyumba ya Ufumu yawo. Zimenezi zimathandiza kuti nyumbayo izikonzedwa pafupipafupi. Zimachititsanso kuti Nyumba ya Ufumu isawonongeke kwambiri ndipo mpingo suwononga ndalama zambiri. (2 Mbiri 24:13; 34:10) Nyumba ya Ufumu ikakhala yoyera komanso yosamalidwa bwino, imakhala malo abwino olambiriramo Mulungu wathu. Choncho tikamathandiza nawo kukonza ndi kusamalira Nyumba yathu ya Ufumu, timasonyeza kuti timakonda Yehova komanso timalemekeza malo athu olambirira. (Salimo 122:1) Zimenezi zimathandizanso kuti anthu amene ayandikira Nyumba ya Ufumu yathu, aziilemekeza.​—2 Akorinto 6:3.

  • N’chifukwa chiyani sitiyenera kunyalanyaza kusamalira malo athu olambirira?

  • Kodi mpingo umakonza zotani kuti Nyumba ya Ufumu yawo izikhala yooneka bwino?