Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 20

Kodi Bungwe Lolamulira Limagwira Ntchito Bwanji Masiku Ano?

Kodi Bungwe Lolamulira Limagwira Ntchito Bwanji Masiku Ano?

Bungwe lolamulira la m’nthawi ya atumwi

Akuwerenga kalata yochokera ku bungwe lolamulira

Mu nthawi ya atumwi, panali kagulu kakang’ono ka “atumwi ndi akulu ku Yerusalemu,” omwe anali ngati bungwe lolamulira. Bungwe limeneli linkasankha zoyenera kuchita pa nkhani zofunika kwambiri zokhudza mpingo wonse wa Akhristu odzozedwa. (Machitidwe 15:2) Iwo akamakambirana, ankagwirizana mfundo imodzi chifukwa ankagwiritsa ntchito Malemba komanso chifukwa chakuti mzimu wa Mulungu unkawatsogolera. (Machitidwe 15:25) Izi n’zimenenso zimachitika masiku ano.

Mulungu akugwiritsa ntchito Bungwe Lolamulira pokwaniritsa chifuniro chake. Abale odzozedwa amene akutumikira m’bungweli amagwira mwakhama kwambiri ntchito yophunzitsa anthu Mawu a Mulungu. Popeza iwo atumikira Mulungu kwa nthawi yaitali, amadziwa bwino kutsogolera ntchito yathu komanso amadziwa bwino kuyankha mafunso okhudzana ndi nkhani zauzimu. Abalewa amakumana mlungu uliwonse kuti akambirane zinthu zokhudza mpingo wachikhristu padziko lonse. Mofanana ndi zomwe zinkachitika m’nthawi ya atumwi, Bungwe Lolamulira limapereka malangizo ochokera m’Baibulo kudzera m’makalata kapena potumiza oyang’anira oyendayenda komanso abale osiyanasiyana kumipingo. Zimenezi zimathandiza kuti anthu a Mulungu aziganiza ndiponso kuchita zinthu mofanana. (Machitidwe 16:4, 5) Bungwe Lolamulira limayang’anira ntchito yokonza chakudya chauzimu, limalimbikitsa anthu kuti aziona ntchito yolalikira za Ufumu kukhala yofunika kwambiri komanso limayang’anira ntchito yoika abale osiyanasiyana pa maudindo mumpingo.

Limatsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. Bungwe Lolamulira limadalira Yehova, Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, komanso Yesu yemwe ndi Mutu wampingo, kuti azilitsogolera. (1 Akorinto 11:3; Aefeso 5:23) Anthu a m’Bungwe Lolamulira sadziona ngati atsogoleri a anthu a Mulungu. Koma iwo limodzi ndi Akhristu onse odzozedwa “amatsatira Mwanawankhosa [Yesu] kulikonse kumene akupita.” (Chivumbulutso 14:4) Abale a m’bungweli amayamikira kwambiri tikamawapempherera.

  • Kodi ndani anali m’bungwe lolamulira m’nthawi ya atumwi?

  • Kodi Bungwe Lolamulira masiku ano limasonyeza bwanji kuti limafunitsitsa kutsogoleredwa ndi Mulungu?