Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 3

Kodi Chinachitika N’chiyani Kuti Choonadi cha M’Baibulo Chidziwikenso?

Kodi Chinachitika N’chiyani Kuti Choonadi cha M’Baibulo Chidziwikenso?

Ophunzira Baibulo, m’ma 1870

Magazini yoyambirira ya Nsanja ya Olonda, mu 1879

Nsanja ya Olonda masiku ano

Baibulo linaneneratu kuti pambuyo pa imfa ya Khristu, mumpingo woyambirira wachikhristu mudzafika aphunzitsi onyenga ndipo adzapotoza choonadi cha m’Baibulo. (Machitidwe 20:29, 30) Patapita nthawi, zimenezi zinachitikadi. Aphunzitsi onyengawa anayamba kusakaniza mfundo zimene Yesu ankaphunzitsa ndi ziphunzitso za chipembedzo chachikunja. Zimenezi n’zomwe zinachititsa kuti pakhale Chikhristu chonyenga. (2 Timoteyo 4:3, 4) Kodi masiku ano tingatsimikize bwanji kuti tikumvetsa bwino mfundo zenizeni zimene Baibulo limaphunzitsa?

Nthawi yoti Yehova aulule choonadi inakwana. Iye analosera kuti ‘m’nthawi yamapeto anthu ambiri adzadziwa zinthu zambiri zoona.’ (Danieli 12:4) M’chaka cha 1870, gulu laling’ono la anthu ofufuza choonadi, linazindikira kuti mfundo zambiri zimene matchalitchi ankaphunzitsa sizinali zogwirizana ndi Malemba. Choncho anayamba kufufuza m’Baibulo kuti adziwe choonadi cha m’Malemba, ndipo Yehova anawadalitsa powathandiza kuti azimvetsa bwino malembawo.

Anthu oona mtima ankaphunzira Baibulo mwakhama. Ophunzira Baibulo akhamawo, ankagwiritsa ntchito njira yabwino kwambiri pophunzira Mawu a Mulungu, ndipo masiku ano tikugwiritsabe ntchito njira imeneyo. Iwo ankaphunzira Baibulo pokambirana mutu wa nkhani umodzi, ndipo akatha ankasankha mutu wina. Koma akapeza nkhani ya m’Baibulo yovuta kumvetsa, iwo ankafufuza mavesi ena amene angawathandize kumvetsa nkhaniyo. Ndiyeno akakambirana nkhaniyo mpaka pamapeto, n’kupeza mfundo imodzi yogwirizana ndi Malemba ena onse, ankailemba penapake. Popeza ankalola kuti Baibulo lizidzitanthauzira lokha, Ophunzira Baibulowo anadziwa choonadi chokhudza dzina la Mulungu komanso Ufumu wake. Anadziwanso chifukwa chimene Mulungu analengera anthu ndi dziko lapansili, zimene zimachitika munthu akamwalira, komanso zoti akufa adzauka. Ntchito yawo yofufuza choonadi inawathandiza kuti amasuke ku miyambo komanso zikhulupiriro zambiri zabodza.—Yohane 8:31, 32.

Pofika mu 1879, Ophunzira Baibulo anazindikira kuti nthawi yafika yoti athandize anthu enanso ambiri kuti adziwe choonadi. Choncho m’chaka chimenechi, iwo anayamba kufalitsa magazini ya Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova, imene tikufalitsabe mpaka pano. Panopa tikuphunzira choonadi cha m’Baibulo ndi anthu m’mayiko 240, m’zinenero zoposa 750. Zoonadi, mosiyana ndi nthawi ina iliyonse m’mbuyomu, panopa anthu ambiri adziwa choonadi.

  • Kodi anthu ena anachita chiyani ndi choonadi cha m’Baibulo pambuyo pa imfa ya Khristu?

  • Kodi n’chiyani chatithandiza kuti tidziwenso choonadi cha m’Mawu a Mulungu?