Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 4

N’chifukwa Chiyani Tinatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano?

N’chifukwa Chiyani Tinatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano?

Congo (Kinshasa)

Rwanda

Kachidutswa ka mpukutu wotchedwa Symmachus kokhala ndi dzina la Mulungu pa Salimo 69:31, ka zaka za m’ma 200 C.E. kapena 300 C.E.

Kwa zaka zambiri, ife a Mboni za Yehova tinkagwiritsa ntchito Mabaibulo osiyanasiyana komanso tinkawasindikiza ndi kuwafalitsa. Koma tinaona kuti pakufunika Baibulo lina limene lingathandize mosavuta munthu aliyense ‘kudziwa choonadi molondola,’ chifukwa ndi zimene Mulungu akufuna. (1 Timoteyo 2:3, 4) Choncho, mu 1950 tinayamba kutulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la chinenero chamakono, ndipo tinkalitulutsa m’zigawozigawo. Baibulo limeneli linamasuliridwa molondola kwambiri ndipo likupezeka m’zinenero zoposa 130.

Pankafunika Baibulo losavuta kumvetsa. Zinenero zimasintha pakapita nthawi yaitali. Choncho m’Mabaibulo ambiri muli mawu omwe anthu anasiya kuwagwiritsa ntchito ndipo ndi ovuta kumvetsa. Komanso anthu apeza mipukutu yakale yolondola kwambiri, imene ikufanana kwambiri ndi mipukutu yoyambirira yeniyeni. Zimenezi zachititsa kuti omasulira Baibulo amvetse bwino zinenero zimene anagwiritsa ntchito polemba Baibulo, monga Chiheberi, Chiaramu, ndi Chigiriki.

Pankafunika Baibulo lomasulira mawu a Mulungu molondola. M’malo mosintha malemba ouziridwa ndi Mulungu, omasulira Baibulo ayenera kumasulira malembawo molondola kwambiri. Koma anthu amene anamasulira Mabaibulo ambiri sanagwiritse ntchito dzina la Mulungu lakuti Yehova, m’Malemba Opatulika.

Pankafunika Baibulo lopereka ulemu kwa Mlembi wake. (2 Samueli 23:2) Baibulo la Dziko Latsopano, linabwezeretsa dzina la Yehova m’malo 7,000 amene limapezeka m’mipukutu yakale kwambiri ya Baibulo, monga momwe chithunzi chili m’munsichi chikusonyezera. (Salimo 83:18) Zinatheka kumasulira Baibulo limeneli chifukwa chakuti, kwa zaka zambiri, anthu ena anagwira mwakhama ntchito yofufuza malemba. Kenako anamasulira Baibulo losavuta kuwerenga, lomwe limafotokoza maganizo a Mulungu momveka bwino kwambiri. Kaya muli ndi Baibulo la Dziko Latsopano m’chinenero chanu kapena ayi, tikukulimbikitsani kuti muziwerenga Mawu a Yehova tsiku lililonse.​—Yoswa 1:8; Salimo 1:2, 3.

  • N’chifukwa chiyani tinaganiza zomasulira Baibulo latsopano?

  • Kodi aliyense amene akufuna kudziwa chifuniro cha Mulungu ayenera kumachita chiyani tsiku lililonse?