Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 GAWO 4

Kudziimba Mlandu—“Ndiyeretseni ku Tchimo Langa”

Kudziimba Mlandu—“Ndiyeretseni ku Tchimo Langa”

Mlongo wina dzina lake Martha anati: “Ndinayamba ntchito ya malipiro abwino koma inachititsa kuti ndiyambe zinthu zina zolakwika. Ndinayamba kuchita nawo zinthu monga khirisimasi, kupezeka pa misonkhano yandale ndipo ndinafika pokalowa m’tchalitchi. Ndinasiya kutumikira Yehova kwa zaka 40. Pamene zaka zinkadutsa ndinayamba kuona kuti Yehova sangandikhululukire. Ndinkangokhalira kudziimba mlandu chifukwa ndinkadziwa bwino mfundo za m’Baibulo koma ndinkachitabe zoipazo.

KUDZIIMBA mlandu kungatifooketse kwambiri. Paja Davide analemba kuti: “Zolakwa zanga zakwera kupitirira mutu wanga. Zandilemera kwambiri ngati katundu wolemera.” (Salimo 38:4) Akhristu ena amadziimba mlandu kwambiri mpaka kufika poganiza kuti Yehova sangawakhululukire. (2 Akorinto 2:7) Koma kodi maganizowa ndi olondola? Ngakhale titachita machimo aakulu kwambiri, kodi n’zoona kuti Yehova sangatikhululukire? Ayi, si zoona.

‘Tiyeni Tikambirane Kuti Mukhalenso pa Ubwenzi ndi Ine’

Yehova sataya anthu ochimwa amene alapa. Iye amafunitsitsa kuti anthu oterewa abwerere. Yesu anafotokoza bwino mfundoyi mu fanizo la mwana wolowerera. Anayerekezera Yehova ndi bambo amene mwana wake anachoka pakhomo n’kukayamba makhalidwe oipa. Koma kenako mwanayo anabwerera. Yesu anati: “[Mwanayo] ali chapatali ndithu, bambo akewo anamuona ndipo anagwidwa chifundo. Pamenepo anamuthamangira ndi kumukumbatira ndipo anamupsompsona mwachikondi.” (Luka 15:11-20) Kodi inuyo mumafuna mutabwerera kwa Yehova koma mukuona kuti muli kutali kwambiri? Dziwani kuti Yehova amakukondani ngati mmene bambo wa mu fanizo lija ankakondera mwana wake. Iye akufunitsitsa kuti mubwerere.

Koma kodi mungatani ngati mukuona kuti machimo anu ndi aakulu kapena ndi ambirimbiri moti Yehova sangakhululuke? Ndi bwino kukumbukira zimene Yehova ananena pa Yesaya 1:18. Iye anati: “Bwerani tsopano anthu inu. Tiyeni tikambirane ndipo ine ndikuthandizani kuti mukhalenso pa ubwenzi wabwino ndi ine. Ngakhale machimo anu atakhala ofiira kwambiri, adzayera kwambiri.” Lembali likusonyeza kuti ngakhale machimo athu atakhala ngati zinthu zofiira zimene zathimbiriritsa chovala choyera, Yehova akhoza kutikhululukira.

Mulungu safuna kuti muzingokhalira kudziimba mlandu. Ndiyeno kodi mungatani kuti Yehova akukhululukireni? Tiyeni tikambirane zinthu ziwiri zimene zinathandiza Davide. Choyamba, iye anati: “Ndidzaulula kwa Yehova machimo anga.” (Salimo 32:5) Ndiyeno kumbukirani kuti Yehova wakuitanani kale kuti ‘mukambirane naye’ n’kukonza ubwenzi wanu ndi iye. Chofunika n’kungochita zimene wanenazi. Ndi bwino kuulula machimo anu kwa Yehova n’kumufotokozera mmene mukumvera. Davide ankadziwa kuti Yehova amuthandiza ndipo anapempha kuti: “Ndiyeretseni ku tchimo langa.” Ananenanso kuti: “Inu Mulungu, simudzanyoza mtima wosweka ndi wophwanyika.”—Salimo 51:2, 17.

Chachiwiri, Davide anathandizidwa ndi mneneri wa Mulungu dzina lake Natani. (2 Samueli 12:13)  Masiku ano, Yehova watipatsanso akulu mumpingo amene aphunzitsidwa bwino zimene angachite pothandiza ochimwa amene alapa kuti akhalenso pa ubwenzi ndi Yehova. Mukawafotokozera vuto lanu, iwo adzakulimbikitsani pogwiritsa ntchito Malemba ndipo adzakupemphererani. Izi zidzathandiza kuti mtima wanu ukhale m’malo, musiye kudziimba mlandu ndiponso muyambe kutumikira Mulungu bwinobwino.—Yakobo 5:14-16.

Yehova sakufuna kuti muzivutika chifukwa chodziimba mlandu

“Wodala Ndi Munthu Amene Wakhululukidwa Zolakwa Zake”

Mwina mukuona kuti kuulula machimo anu kwa Yehova ndiponso kupempha akulu kuti akuthandizeni n’kovuta kwambiri. Kumbukirani kuti zimenezi zinachitikiranso Davide. Iye “anakhala chete” kwa kanthawi ndithu osaulula. (Salimo 32:3) Kenako anaona ubwino wa kuulula machimo ake ndiponso kukonza ubwenzi wake ndi Mulungu.

Davide ataulula machimo ake anayambanso kusangalala. Iye analemba kuti: “Wodala ndi munthu amene wakhululukidwa zolakwa zake, amene machimo ake aphimbidwa.” (Salimo 32:1) Anapempheranso kuti: “Inu Yehova, tsegulani milomo yangayi, kuti pakamwa panga patamande inu.” (Salimo 51:15) Choncho atakhululukidwa machimo ake, Davide ankafunitsitsa kuuza ena za Yehova.

Yehova sakufuna kuti muzivutika chifukwa chodziimba mlandu. Koma akufuna kuti mukhale osangalala komanso ofunitsitsa kulalikira za iye. (Salimo 65:1-4) Paja akufunanso kuti ‘machimo anu afafanizidwe, ndiponso kuti nyengo zotsitsimutsa zibwere kuchokera kwa iye.’—Machitidwe 3:19.

Izitu n’zimene zinachitikira mlongo amene tamutchula kumayambiriro uja. Iye anati: “Mwana wanga wamwamuna ankanditumizira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ndiyeno pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kukonza ubwenzi wanga ndi Yehova. Zinandivuta kwambiri kuti ndipemphe Yehova kundikhululukira machimo anga onse. Koma ndinalimba mtima n’kumupempha kuti andikhululukire. Sindikumvetsa kuti panapita zaka 40 ndisanabwerere kwa Yehova. Izitu zikusonyeza kuti ngakhale munthu atasiya kutumikira Yehova kwa zaka zambiri, akhoza kubwerera n’kukonzanso ubwenzi wake ndi iye.”