Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 16

Sonyezani Chikondi Chanu kwa Mulungu

Sonyezani Chikondi Chanu kwa Mulungu

Kuti musataye bwenzi lanu, muyenera kumalankhula naye. Mumamvetsera kwa iye, iyenso amamvetsera kwa inu. Mumauzanso anthu ena zabwino za bwenzi lanulo. N’chimodzimodzinso mukakhala bwenzi la Mulungu. Talingalirani zimene Baibulo limanena pankhaniyi:

Lankhulani ndi Yehova m’pemphero nthaŵi zonse. “Limbikani chilimbikire m’kupemphera.”—Aroma 12:12.

Ŵerengani Mawu a Mulungu, Baibulo. “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.”—2 Timoteo 3:16.

Phunzitsani ena za Mulungu. “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, . . . ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.”—Mateyu 28:19, 20.

 Khalani pafupi ndi mabwenzi a Mulungu. “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru.”—Miyambo 13:20.

Fikani pamisonkhano pa Nyumba ya Ufumu. “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino.”—Ahebri 10:24, 25.

Chirikizani ntchito ya Ufumu. “Yense [apatse] monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.”—2 Akorinto 9:7.