Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 10

Mmene Mungapezere Chipembedzo Choona

Mmene Mungapezere Chipembedzo Choona

Ngati mufuna kukhala bwenzi la Mulungu, muyenera kuloŵa chipembedzo chimene Mulungu amavomereza. Yesu anati “olambira oona” adzalambira Mulungu mogwirizana ndi “choonadi.” (Yohane 4:23, 24) Pali njira yolondola imodzi yokha yolambirira Mulungu. (Aefeso 4:4-6) Chipembedzo choona chimatsogolera ku moyo wosatha, koma chipembedzo chonyenga chimatsogolera ku chiwonongeko.—Mateyu 7:13, 14.

Mukhoza kuzindikira chipembedzo choona mwa kuona mmene anthu ake amakhalira. Popeza Yehova ndi wabwino, olambira ake oona ayeneranso kukhala anthu abwino. Monga mmene mtengo wabwino wa malalanje umaberekera zipatso zokoma, chipembedzo choonanso chimakhala ndi anthu abwino.—Mateyu 7:15-20.

Mabwenzi a Yehova amalemekeza kwambiri Baibulo. Amadziŵa kuti Baibulo linachokera kwa Mulungu. Amalola zimene limanena kutsogolera miyoyo yawo, pothetsa mavuto awo, ndi kuwathandiza kuphunzira za Mulungu. (2 Timoteo 3:16) Amayesetsa kuchita zimene amalalikira.

 Mabwenzi a Yehova amasonyezana chikondi. Yesu anasonyeza chikondi kwa anthu mwa kuwaphunzitsa za Mulungu ndi mwa kuchiritsa odwala. Ajanso amene amachita chipembedzo choona amasonyeza chikondi kwa ena. Mofanana ndi Yesu, iwo sanyoza osauka kapena a mtundu wina. Yesu anati anthu adzadziŵa ophunzira ake mwa chikondi chimene amasonyezana wina ndi mnzake.—Yohane 13:35.

Mabwenzi a Mulungu amalemekeza dzina la Mulungu, Yehova. Ngati munthu wina akana kutchula dzina lanu, kodi mungati ameneyo ndi bwenzi lanu lenileni? Ayi! Pamene tili ndi bwenzi, timatchula dzina lake ndipo timauza anthu ena zabwino za bwenzi lathulo. Choncho, aja ofuna kukhala mabwenzi a Mulungu ayenera kumatchula dzina lake ndi kumauzanso ena za iye. N’zimene Yehova amafuna kuti tizichita zimenezo.—Mateyu 6:9; Aroma 10:13, 14.

Mofanana ndi Yesu, mabwenzi a Mulungu amaphunzitsa ena za Ufumu wa Mulungu. Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba limene lidzakonza dziko lapansi kukhala paradaiso. Mabwenzi a Mulungu amauzako anthu ena za uthenga wabwino umenewu wonena za Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 24:14.

Mboni za Yehova zimayesetsa kukhala mabwenzi a Mulungu. Iwo amalemekeza Baibulo ndipo amakondana kwambiri. Amatchula dzina la Mulungu ndi kulilemekeza, ndipo amaphunzitsanso anthu ena za Ufumu wa Mulungu. Mboni za Yehova zili ndi chipembedzo choona padziko lapansi lero.