Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 1

Mulungu Akukuitanani Kuti Mukhale Bwenzi Lake

Mulungu Akukuitanani Kuti Mukhale Bwenzi Lake

Mulungu akufuna kuti mukhale bwenzi lake. Kodi munayamba mwaganizapo zakuti mukhoza kukhala bwenzi la Munthu wamkulu kopambana m’chilengedwe chonse? Abrahamu, amene anakhalapo ndi moyo kalekale, anatchedwa bwenzi la Mulungu. (Yakobo 2:23) Anthu enanso osimbidwa m’Baibulo anali paubwenzi wabwino ndi Mulungu ndipo anadalitsidwa kwambiri. Lerolino, anthu ena m’madera onse a dziko lapansi akhala mabwenzi a Mulungu. Inunso mutha kukhala bwenzi la Mulungu.

Ubwenzi ndi Mulungu umaposa ubwenzi ndi munthu wina aliyense. Mulungu sagwiritsa mwala mabwenzi ake okhulupirika. (Salmo 18:25) Ubwenzi ndi Mulungu umaposa ngakhale kukhala ndi chuma chambiri. Munthu wachuma akamwalira, chuma chakecho chimapita kwa ena. Komabe, aja amene ali ndi ubwenzi wabwino ndi Mulungu, ali ndi chuma chimene wina aliyense sangawalande.—Mateyu 6:19.

Anthu ena angayese kukuletsani kuphunzira za Mulungu. Ngakhale ena a mabwenzi anu kapena apabanja lanu angachite zimenezi. (Mateyu 10:36, 37) Ngati ena akusekani kapena kukuopsezani, dzifunseni kuti, ‘Kodi ndikufuna kukondweretsa ndani—anthu kapena Mulungu?’ Taganizirani izi: Ngati munthu wina akuuzani kuti musiye kudya, kodi mungamumvere ameneyo? Kutalitali! Mufunikira chakudya kuti mukhale ndi moyo. Koma Mulungu akhoza kukupatsani moyo wosatha! Choncho, musalole wina aliyense kuti akuletseni kuphunzira za mmene mungakhalire bwenzi la Mulungu.—Yohane 17:3.