Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 12

N’chiyani Chimachitika pa Imfa?

N’chiyani Chimachitika pa Imfa?

Pali imfa palibe moyo. Imfa ili ngati tulo tofa nato. (Yohane 11:11-14) Akufa satha kumva, kuona, kulankhula, kapena kuganiza chilichonse. (Mlaliki 9:5, 10) Chipembedzo chonyenga chimaphunzitsa kuti akufa amapita kudziko la mizimu kukakhala limodzi ndi mizimu ya makolo awo. Baibulo siliphunzitsa zimenezo.

Anthu akufa sangatithandize, ndiponso sangativulaze. Nthaŵi zambiri anthu amachita miyambo inayake ndi kupereka nsembe zimene amakhulupirira kuti zimakondweretsa akufawo. Zimenezi zimam’nyansa Mulungu chifukwa zimachokera pa limodzi la mabodza a Satana. Ndipo sizikondweretsa ngakhale akufawo, chifukwa iwo alibe moyo. Sitiyenera kuopa akufa kapena kuwalambira. Tiyenera kulambira Mulungu yekha.—Mateyu 4:10.

Akufa adzakhalanso ndi moyo. Yehova adzaukitsa akufa kuti adzakhalenso ndi moyo padziko lapansi la paradaiso. Nthaŵiyo idakali m’tsogolo. (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15) Mulungu akhoza kuukitsa akufa monga momwe mungagalamutsire munthu amene ali m’tulo.—Marko 5:22, 23, 41, 42.

Ganizo lakuti anthufe sitifa ndi bodza lamkunkhuniza lofalitsidwa ndi Satana Mdyerekezi. Satana ndi ziŵanda zake amapangitsa anthu kuganiza kuti mizimu ya akufa ndi yamoyo ndipo imachititsa matenda ndi mavuto ena. Satana amanyenga anthu, nthaŵi zina kudzera m’maloto ndi masomphenya. Yehova amadana ndi anthu amene amayesa kulankhula ndi akufa.—Deuteronomo 18:10-12.