Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 13

Matsenga ndi Ufiti ndi Zoipa

Matsenga ndi Ufiti ndi Zoipa

Satana amafuna kuti muzichita zamatsenga. Anthu ambiri amapereka nsembe kwa makolo awo akufa kapena mizimu yawo pofuna kudziteteza kuti isawavulaze. Amachita zimenezo poopa mphamvu ya mizimu ya akufa. Iwo amavala mphete kapena makhoza amatsenga. Amamwa kapena kufikisa m’thupi “mankhwala” amene amakhulupirira kuti ali ndi mphamvu zamatsenga. M’nyumba zawo kapena pansi m’thaka, anthu ena amabisa mankhwala omwe amakhulupirira kuti ali ndi mphamvu yoteteza. Ena amagwiritsa ntchito “mankhwala” amatsenga pokhulupirira kuti adzawatheketsa kupambana pabizinesi, pamayeso akusukulu, kapena paubwenzi wawo ndi munthu amene afuna kumanga naye banja.

Chitetezo chanu chopambana polimbana ndi Satana ndicho ubwenzi ndi Yehova. Yehova Mulungu limodzi ndi angelo ake ndi amphamvu kwambiri kuposa Satana ndi ziŵanda zake. (Yakobo 2:19; Chivumbulutso 12:9) Yehova amafunitsitsa kusonyeza mphamvu yake poteteza mabwenzi ake—aja okhulupirika kwathunthu kwa iye.—2 Mbiri 16:9.

Mawu a Mulungu amati: “Musamachita . . . kuombeza ula.” Yehova amadana ndi zamatsenga ndi ufiti chifukwa zimaika munthu mwachindunji m’mphamvu ya Satana Mdyerekezi.—Levitiko 19:26.