Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 DOMINICAN REPUBLIC

Munthu Woyamba wa Chinenero Chamanja Kuphunzira Baibulo

José Pérez

Munthu Woyamba wa Chinenero Chamanja Kuphunzira Baibulo
  • KUBADWA 1960

  • KUBATIZIDWA 1982

  • MBIRI YAKE Ali mnyamata ankakonda kwambiri Mulungu chifukwa chakuti abale ankamusonyeza chikondi ngakhale kuti iwo sankadziwa Chinenero Chamanja.

Ndinagontha ndili mwana ndipo ndinkapita kusukulu yophunzitsa Chinenero Chamanja. Ndili ndi zaka 11, ndinakumana ndi wa Mboni za Yehova ndipo anandiitanira ku misonkhano. Nditapita, sindinamveko chilichonse koma ndinangoona kuti anthu ake andilandira bwino kwambiri ndipo ndinaganiza zoti ndizisonkhanabe. Anthu ambiri mumpingomo ankandiitana kuti tikadye komanso tikacheze.

Mu 1982, ndinakhala wofalitsa ndipo chakumapeto kwa chakachi ndinabatizidwa. Mu 1984 ndinakwatira Eva, ndipo nayenso amangomva Chinenero Chamanja basi. Kunena zoona sitinkamvetsa mfundo zambiri za m’Baibulo koma chikondi chimene abale ankatisonyeza chinatitsimikizira kuti tapeza gulu la Yehova.—Yoh. 13:35.

Mu 1992, panakonzedwa zoti abale ndi alongo aphunzitsidwe  Chinenero Chamanja cha ku America. Abale ndi alongo amene anaphunzitsidwawo anayamba kufufuza anthu ndiponso kuwaphunzitsa uthenga wabwino. Ndiyeno mu 1994, banja lina la ku Puerto Rico linaitanidwa kunthambi kuti liphunzitse abale ndi alongo 25 Chinenero Chamanja. Apa tsopano zinthu zinayamba kuyenda bwino m’gawo la chinenerochi.

Chakumapeto kwa chakachi kagulu ka chinenerochi kanakhazikitsidwa ndipo ine ndi Eva tinkasonkhana kumeneko. Titayamba kusonkhana kumeneku m’pamene tinamvetsa nkhani zina monga zoti Satana anatsutsa ulamuliro wa Yehova komanso zoti Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumu wa Mesiya pokwaniritsa cholinga chake.

Pa December 1, 1995, mipingo ya Chinenero Chamanja cha ku America inakhazikitsidwa ku Santo Domingo ndi ku Santiago. Pofika mu August 2014, m’dzikoli munali mipingo 26 ya chinenero chamanja ndiponso timagulu 18.

Ine ndi Eva tinkangolankhula ndi ana athu Chinenero Chamanja. Mwana wathu woyamba dzina lake Éber amathandiza kumasulira Chinenero Chamanja kunthambi ya ku United States. Ine ndine mtumiki wothandiza ndipo mkazi wanga ndi mpainiya wokhazikika.