Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 DOMINICAN REPUBLIC

“Ufumu wa Mulungu Si Nkhambakamwa”

Efraín De La Cruz

“Ufumu wa Mulungu Si Nkhambakamwa”
  • CHAKA CHOBADWA 1918

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1949

  • MBIRI YAKE Ngakhale kuti anatsekeredwa m’ndende 7 ndipo ankamenyedwa koopsa, sanasiye kulalikira mwakhama uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.

MU 1948, ine ndi mkazi wanga Paula limodzi ndi mwana wathu tinayamba kupita ku misonkhano ya Mboni za Yehova m’dera la Blanco Arriba. Tinkayenda ulendo wa makilomita 40 kupita n’kubwera koma sitinkajomba ku misonkhano. Ndiyeno ine ndi Paula tinabatizidwa pa January 3, 1949.

Patapita miyezi 6, ine limodzi ndi anthu ena mumpingo wathu tinamangidwa ndipo anatilamula kuti tikhale m’ndende kwa miyezi itatu. Tinkagona pansi ndipo ankatipatsa nthochi ndi tiyi kamodzi pa tsiku. Titamasulidwa, akuluakulu a boma anatiopseza ndipo ankaona ngati tisiya kulalikira. Koma titabwerera kwathu tinapitiriza kusonkhana ndiponso kulalikira mosamala. Tinkasonkhana m’nyumba za abale, m’minda ya khofi ndiponso kumafamu chifukwa chakuti apolisi ankatisakasaka. Sitinkasonkhana pamalo amodzimodzi ndipo tikamaliza misonkhano tinkalengeza malo odzachitira misonkhano yotsatira. Polalikira, aliyense ankakhala yekha ndipo tinkavala  zovala zogwirira ntchito. Komanso sitinkagwiritsa ntchito mabuku kapena Baibulo. Ngakhale kuti ndinkasamala kwambiri, kuyambira mu 1949 mpaka mu 1959, ndinamangidwa mobwerezabwereza. Ndinatsekeredwa m’ndende 7 ndipo nthawi iliyonse ndinkakhalamo miyezi itatu kapena 6.

Ndinkachita zinthu mosamala kwambiri chifukwa anthu ena amene ankandizunza anali achibale anga. Ngakhale kuti ndinkayesetsa kuwazemba pogona kumapiri kapena pafamu inayake, nthawi zina ankandigwira. Nthawi ina ndinatsekeredwa m’ndende ya La Victoria ku Ciudad Trujillo ndipo muselo imodzi tinkakhalamo anthu 50 kapena 60. Tinkapatsidwa phala m’mawa ndipo masana tinkapatsidwa mpunga wochepa ndi nyemba. Abalefe tinkalalikira anthu ena m’ndendemo komanso tinkachita misonkhano nthawi zonse. Pa misonkhanoyo, tinkakambirana malemba amene tinawaloweza komanso kufotokoza zimene tinkakumana nazo mu utumiki.

Nthawi yomaliza imene ndinamangidwa, msilikali wina anandimenya ndi mfuti m’mutu ndiponso m’nthithi. Ndimavutikabe chifukwa chomenyedwa ndiponso kuzunzidwa. Koma zimene ndinakumana nazozo zinandithandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba, kukhala wopirira komanso kutumikira Yehova mosabwerera m’mbuyo.

Panopa ndili ndi zaka 96 ndipo ndine mtumiki wothandiza mumpingo wathu. Sindingathe kupita kutali koma ndimakhala pafupi ndi nyumba yanga n’kumalalikira anthu amene akudutsa. Ndimadziwa kuti Ufumu wa Mulungu si nkhambakamwa ayi. Ndakhala ndikulalikira za Ufumuwo kwa zaka zoposa 60. Nditangomva za dziko latsopano ndinakhulupirira kwambiri kuti libweradi ndipo mpaka pano ndikukhulupirira zimenezo. *

^ ndime 3 Efraín De La Cruz anamwalira nkhaniyi ikulembedwa.