Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 DOMINICAN REPUBLIC

Panafunika Olalikira Ufumu Ambiri

Panafunika Olalikira Ufumu Ambiri

Uthenga Wabwino Unafika M’madera Akumidzi

Amishonale ambiri anafika ku Dominican Republic. Mayina awo anali Pete Paschal, Amos ndi Barbara Parker, Richard ndi Belva Stoddard, amene anatumikira ku Bolivia, ndiponso Jesse ndi Lynn Cantwell ochokera ku Colombia. Amishonalewa anathandiza kwambiri kuti ntchito yolalikira iziyenda bwino. Pofika mu 1973, ntchitoyi inkagwirika kwambiri m’matauni ndi m’mizinda osati m’madera akumidzi. Ndiyeno panakonzedwa dongosolo loti anthu akumidzi athandizidwenso. Abale ndi alongo anapemphedwa kuti akalalikire kumidzi kwa miyezi iwiri ndipo apainiya okhazikika 19 anadzipereka. Kuchokera mu December 1973 kufika mu January 1977, apainiyawo anatumizidwa m’madera amene uthenga wabwino unali usanafike.

“Tinkasinthanitsa mabuku athu ndi nkhuku, mazira ndi zipatso”

Mpainiya wina amene anagwira nawo ntchitoyi anati: “Tinkalalikira tsiku limodzi ndipo mawa lake tinkabwerera kwa anthu amene anasonyeza chidwi. Anthu ambiri analibe ndalama, choncho tinkangosinthanitsa mabuku athu ndi zinthu monga nkhuku, mazira ndi zipatso. Timathokoza Yehova chifukwa chotithandiza kuti tizipeza chakudya.” Kwa anthu ena, kanali koyamba kumva uthenga wa m’Baibulo. M’madera ena, atsogoleri azipembedzo ankauza anthu kuti Yehova ndi Mdyerekezi. Koma anthuwo ankadabwa akawerenga m’Baibulo malemba monga Salimo 83:18  limene limati: “Inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.” M’madera ena anthu ambiri ankachita chidwi moti nthawi yomweyo pankakonzedwa zoti kuzichitika misonkhano.

Kunabwera Amishonale Ena Ndipo Nthambi Yatsopano Inamangidwa

Mu September 1979, Abigail Pérez ndi mkazi wake dzina lake Georgina anafikanso m’dzikoli. Iwo anauzidwa kuti agwire ntchito yoyang’anira dera. Mu 1987, Tom ndi Shirley Dean atamaliza maphunziro a ku Giliyadi anatumizidwanso m’dzikoli. Kunabweranso atumiki a nthawi zonse apadera ochokera ku Puerto Rico. Mu August 1988, Reiner ndi Jeanne Thompson anatumizidwanso ku Dominican Republic, ndipo ili linali dziko la nambala 5 limene anakachita umishonale.

Pofika mu 1989, ku Dominican Republic kunali ofalitsa 11,081 ndipo zinkaoneka kuti awonjezekabe chifukwa anachitira lipoti maphunziro okwana 20,494. Kuwonjezekaku kunali ndi mavuto ake. Mwachitsanzo, pofika m’ma 1980, nthambi inayamba kuchepa chifukwa kunali anthu ambiri. M’bale Reiner Thompson anati: “Malo anacheperatu moti tinkafunika kupeza nyumba zina kuti anthu ena azikakhalamo komanso zina kuti tizikasungamo zinthu.”

“Zinali zovuta kuti tipeze malo omangapo nthambi yatsopano. Kenako munthu wina wa bizinezi atamva zoti tikufuna malo ananena kuti ali ndi malo abwino kwambiri amene angagulitse kwa Mboni za Yehova zokha basi. Iye anali ndi kampani yosoka zovala ndipo  sekilitale wake komanso antchito angapo anali a Mboni. Iye anaona kuti a Mboniwo anali okhulupirika ndiponso aulemu. Izi zinachititsa kuti azilemekeza kwambiri Mboni za Yehova ndipo anafuna kuti malo akewo agulitse motchipa kwa a Mboniwo.” Malowo anagulidwa mu December 1988, ndipo patapita nthawi tinagulanso malo ena ozungulira. Malo onse anali okwana maekala 22 ndipo tinamangapo nthambi ndi Malo a Misonkhano.

Abale ndi alongo ochokera m’mayiko osiyanasiyana anadzipereka kudzamanga nawo nthambi ndi Malo a Misonkhanowo. Zinthuzi zinatseguliridwa mu November 1996 ndipo kunabwera abale atatu a m’Bungwe Lolamulira. Kunabwera Carey Barber, Theodore Jaracz ndi Gerrit Lösch. Mwambowu unachitika Loweruka ndipo Lamlungu kunalinso mapulogalamu apadera m’masitediyamu akuluakulu a m’dzikoli ndipo anthu oposa 10,000 anaona malo.

‘Anawolokera ku Makedoniya’

Pali nkhani ina yokhudza Mboni za Yehova ku Dominican Republic imene tiyenera kukambirananso. Abale ndi alongo ambirimbiri anasamukira m’madera osiyanasiyana a dzikoli kumene kunalibe ofalitsa ambiri. Atamva zoti m’dzikoli abale amatha kukhala ndi maphunziro ambirimbiri, anthu ena anaganiza zosamukirako cha m’ma 1980. Tingati anthuwo anaganiza ‘zowolokera ku Makedoniya.’ (Mac. 16:9) Anthu amene anasamukawa ankauzanso anzawo mmene utumiki unkayendera bwino ndipo izi zinachititsa kuti cha m’ma 1990 kufike anthu ambirimbiri.

Stevan Norager ndi mkazi wake Miriam anabwera m’dzikoli kuchokera ku Denmark mu 2001 ndipo adakali  komweko. Poyamba, Miriam ndi mchemwali wake anatumira m’dzikoli, ndiyeno atakwatiwa anaganiza zobwererako. Kodi n’chiyani chinawalimbikitsa kusamuka ngakhale kuti chikhalidwe komanso chilankhulo cha m’dzikoli chinali chosiyana ndi chawo? Miriam anati: “Ine ndi mwamuna wanga timachokera m’mabanja ochita bwino mwauzimu. Makolo athu anakhalapo apainiya apadera kenako anafe titabadwa anakhala apainiya okhazikika. Makolo athuwo ankatilimbikitsa kuchita utumiki wa nthawi zonse n’cholinga choti tipatse Yehova zonse zimene tingathe.”

Stevan ndi Miriam akhala akuchita upainiya wapadera m’dzikoli kuyambira mu 2006 ndipo athandiza anthu ambiri kuyamba kutumikira Yehova. Stevan anati: “Tapeza madalitso ankhaninkhani. Mavuto amene  timakumana nawo ndi ochepa tikayerekezera ndi chisangalalo chimene timakhala nacho chifukwa chothandiza anthu ambiri kudziwa Yehova n’kumamukonda kwambiri. Tapezanso anzathu ambirimbiri amene amatikonda. Chifukwa chotumikira kuno, taphunzira kudzichepetsa ndi kuleza mtima. Moyo wosalira zambiri watithandizanso kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova.”

Jennifer Joy watumikira m’dzikoli kwa zaka zoposa 20 ndipo amathandiza m’gawo la Chinenero Chamanja

Mlongo wina wosakwatiwa dzina lake Jennifer Joy akutumikiranso ku Dominican Republic. Azakhali ake, dzina lawo a Edith, ankachita umishonale m’dzikoli ndipo mlongoyu anabwera kudzawaona mu 1992. Iye anaona kuti utumiki m’dzikoli ndi wosangalatsa kwambiri  ndipo anakumana ndi alongo ambirimbiri amene anasamukira m’dzikoli. Jennifer anati: “Munthune ndi wamanyazi komanso ndimadzikayikira. Koma ndinkadziuza kuti, ‘Bola kungoyesa, mwina nanenso ndikwanitsa.’”

Jennifer ankaganiza kuti adzangokhalako kwa chaka chimodzi koma pano watumikira m’dzikoli kwa zaka zoposa 20. Iye wathandiza anthu ambirimbiri kuyamba kutumikira Yehova. Wathandizanso kuti anthu ayambe kulalikira m’Chinenero Chamanja komanso kukonza mabuku ophunzitsira chinenerochi.

‘Yehova wakhala akundisamalira mpaka pano ndiye palibe chifukwa chondichititsa kukayikira zoti andisamaliranso chaka chamawa.’

Kodi Jennifer amapeza bwanji ndalama zogulira zina ndi zina? Iye anati: “Chaka chilichonse ndimapita kwathu ku Canada kukagwira ntchito kwa miyezi yochepa. Ntchito zimene ndimagwira ndi monga kujambula anthu, kukonza zithunzi zimene ndajambula, kupenta nyumba, kuyeretsa m’maofesi, kukonza magetsi a magalimoto ndiponso kukonza makapeti. Ndimagwiranso ntchito yolandira alendo, kuphunzitsa Chingelezi ndiponso kumasulira.” Jennifer amaona kuti moyo wake ukufanana ndi wa Aisiraeli m’chipululu. Iye anati: “Paja Aisiraeli ankakhala ndi moyo chifukwa cha mawu a Yehova. Paja mawu a Yehova ndi amene ankachititsa kuti apeze zonse zofunika monga chakudya cha tsiku lililonse ndipo zovala ndi nsapato zawo sizinathe. (Deut. 8:3-4) Yehova walonjeza kuti azitisamaliranso. (Mat. 6:33) Wakhala akundisamalira mpaka pano ndiye palibe chifukwa chondichititsa kukayikira zoti andisamaliranso chaka chamawa.”

 Ku Dominican Republic kwabwera Akhristu akhama okwana 1,000 ochokera m’mayiko monga Austria, Japan, Poland, Puerto Rico, Russia, Spain, Sweden, Taiwan ndiponso ku United States. Anthu osamukira m’derali ochokera m’mayiko okwana 30 ali m’mipingo ya Chinenero Chamanja cha ku America, Chitchainizi, Chingelezi, Chikiliyo cha ku Haiti, Chirasha ndiponso Chisipanishi. Mofanana ndi Petulo nawonso anasiya zinthu zonse n’kumatsatira Khristu.—Maliko 10:28.