Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 DOMINICAN REPUBLIC

Ntchito Yolalikira Inapitirirabe

Ntchito Yolalikira Inapitirirabe

Amishonale Ankagwirabe Ntchito Mobisa

Zinthu zinayamba kuvuta kwambiri pamene ntchito yathu inaletsedwa. Mlongo wina dzina lake Alma Parson ankachita umishonale ndipo anati: “Nyumba za Ufumu zathu zinatsekedwa ndipo sankatilola kulalikira. Abale athu anakumana ndi mavuto osaneneka.” Ena  anachotsedwa ntchito ndipo ena anamangidwa. Koma mlongoyu ananenanso kuti: ‘Nthawi zambirimbiri tinkachita kuoneratu kuti Yehova akutiteteza ndiponso kutitsogolera.’ Abale ankadalira kwambiri Yehova ndipo ankagwirabe ntchito mobisa.

M’bale Lennart Johnson anafotokoza zimene zinkachitika pamene abale ankaletsedwa kusonkhana. Iye anati: “Abale ankakumana m’timagulu ting’onoting’ono m’nyumba zawo. Tinkaphunzira nkhani za mu Nsanja ya Olonda zimene tinkazikopera pogwiritsa ntchito makina enaake. Akhristu ambiri okhulupirika ankayamikira kwambiri Yehova chifukwa cha mfundo zolimbikitsa zimene tinkaphunzira m’timaguluti.”

Roy Brandt ndi mkazi wake Juanita anatsala m’dzikoli nthawi ya bani

Boma linapitiriza kusakasaka komanso kuzunza abale ndi alongo. Koma iwo sanachite mantha. Pa September 15, 1950, nduna ina mu ofesi ya pulezidenti inauza pulezidenti kuti: “Bambo Lee Roy Brandt ndiponso akuluakulu anzawo amene akutsogolera gulu la Mboni za Yehova sakusintha. Takhala tikuwaitana kambirimbiri n’kuwauza kuti asiye kuphunzitsa anthu zinthu zokhudza chipembedzo chimene chinaletsedwa m’dzikoli koma sakumva. Tsiku lililonse tikulandira malipoti ochokera m’madera osiyanasiyana onena kuti akuchitabe zimenezi mobisa ndiponso akumanyoza boma.” Pomaliza, ndunayi inalimbikitsa pulezidentiyo kuti ndi bwino kuthamangitsa m’dzikolo akuluakulu a gulu la Mboni za Yehova amenewa.

Amishonale Analimbikitsa Kwambiri Abale

Chakumapeto kwa 1950, M’bale Knorr ndi M’bale Henschel anafika m’dzikoli. Ndiyeno amishonale ena  anatumizidwa kuti Argentina, ku Guatemala ndi ku Puerto Rico. Ena anangopeza ntchito n’cholinga choti akhalebe m’dzikolo. Mwachitsanzo, M’bale Brandt anapeza ntchito pa kampani ya zamagetsi koma amishonale ena anayamba ntchito yophunzitsa Chingelezi. Lipoti la mu Buku Lapachaka la 1951 linayamikira amishonalewa kuti: “M’malo mothawa, amishonale ena akukhalabe m’dzikoli. Zimenezi zikulimbikitsa kwambiri Akhristu amene anawaphunzitsa Baibulo. Onse amasangalala akaganizira kulimba mtima kwawo.”

‘Amishonale amene anakhalabe m’dzikoli analimbikitsa kwambiri Akhristu’

Mmishonale wina amene ankaphunzitsa Chingelezi anali Dorothy Lawrence. Koma iye ankaphunzitsanso anthu ena Baibulo. Izi zinachititsa kuti athandize anthu ambiri kukhala a Mboni za Yehova.

Abale okhulupirika anapezanso njira zina zothandiza kuti azilalikira pa nthawi yovutayi. Mwachitsanzo, ankathothola mapepala m’mabuku ena n’kupindapinda kuti akwane m’thumba kapena m’zikwama zimene ankatenga popita kumsika kuti asamakayikiridwe polalikira. Ankalemba malipoti ngati kuti akulemba zinthu zoti akagule kumsika. M’malo molemba kuti mabuku, timabuku, magazini, maulendo obwereza komanso maola,  ankalemba kuti mapapaya, nyemba, mazira, kabichi ndi spinachi. Magazini a Nsanja ya Olonda amene ankawakopera ankangowatchula kuti chinangwa.

Ntchito Yophunzitsa Anthu Inapitirira

Pa June 16, 1954, Rafael Trujillo anasaina pangano ndi akuluakulu a Katolika ku Rome. Panganoli linali lopereka mwayi wapadera kwa ansembe a ku Dominican Republic. Pa nthawiyi n’kuti lamulo loletsa ntchito ya Mboni za Yehova litakhalapo kwa zaka pafupifupi 4. Koma pofika mu 1955, m’dzikoli munali ofalitsa 478. Kodi zinatheka bwanji kuti anthu awonjezeke pa nthawi yovutayi? Lipoti la mu Buku Lapachaka la 1956 linati: “Mzimu wa Yehova ndi umene ukutipatsa mphamvu. Abale athu ndi ogwirizana, chikhulupiriro chawo n’cholimba kwambiri ndipo akupitirizabe molimba mtima.”

Mu July 1955, abale a kulikulu lathu analemba kalata yopita kwa Trujillo. M’kalatayo anafotokoza maganizo a Mboni za Yehova pa nkhani za ndale ndipo anamupempha kuti achotse lamulo loletsa ntchito ya Mboni  za Yehova komanso ya bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society. Kodi zotsatira zake zinali zotani?