Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 DOMINICAN REPUBLIC

“Ndinkamenya Nkhondo Ngati Mkango”

Luis Eduardo Montás

“Ndinkamenya Nkhondo Ngati Mkango”
  • CHAKA CHOBADWA 1906

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1947

  • MBIRI YAKE Anali ndi udindo m’chipani cha Rafael Trujillo. Koma anaphunzira Baibulo n’kukhala wa Mboni za Yehova ndipo anamwalira m’chaka cha 2000 atatumikira Yehova mokhulupirika.

LUIS anali wachibale wa Trujillo ndipo anali msungichuma wa chipani cha Dominican (Partido Dominicano). Iye ankanyansidwa kwambiri ndi ulamuliro wa Trujillo ndipo ankafuna kutula pansi udindo wake koma pulezidentiyu sankamulola kusiya.

Pulezidentiyu anapha azichimwene awiri a Luis. Izi n’zimene zinamuchititsa kuti ayese kupha pulezidentiyo. Palibe anatulukira mapulani ake. Iye anapita kwa asing’anga angapo kuti amuthandize kupha pulezidenti. Luis ananena kuti pulezidentiyu “ankachita ngati chilombo chakutchire ndipo ankadziona ngati wapamwamba kuposa aliyense.” M’nyumba ya sing’anga wina, Luis anaona buku lakuti “The Truth Shall Make You Free” ndipo anayamba kuliwerenga. Bukulo linamusangalatsa kwambiri moti anapita nalo kunyumba. Kenako anazindikira kuti bukulo ndi la chipembedzo choona chomwe ankachifunafuna.

 Luis atapita ku Ciudad Trujillo, anakapezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova ndipo analandira mabuku ndi magazini. Iye anachezera usiku wonse kuwerenga mabukuwo ndipo kenako anapempha kuti aziphunzira Baibulo. Ataphunzira zambiri, anaganiza zosiya ndale. Pulezidenti atamva zimenezi anamunyengerera kuti amupatsa udindo waukulu wokakhala kazembe ku Puerto Rico. Koma Luis anakana ngakhale kuti ankadziwa kuti izi zichititsa kuti azunzidwe.

Luis anati: “Akuluakulu a boma ankayesa kundikopa m’njira zosiyanasiyana. Koma ndinasankha kusiya zosangalatsa za m’dzikoli. Chifukwa cha zimenezi, munthune ndinazunzidwa koopsa.” Iye ankalalikira mwakhama kwambiri moti ansembe ena akatolika ankangomunena kuti “Mlaliki.” Ndiyeno Luis anabatizidwa pa October 5, 1947 patangotha miyezi 6 kuchokera pamene anafika koyamba pa misonkhano.

Iye atangobatizidwa ankasakidwasakidwa, kumangidwa komanso kutsekeredwa muselo yayekha. Anthu anayesa kangapo kuti amuphe. Koma iye akagwidwa n’kufika mukhoti ankaona kuti ndi mwayi woti alalikire. Luis anati: “Ndinkamenya nkhondo ngati mkango poteteza chikhulupiriro changa. Ndikakumbukira, ndimasangalala kwambiri.”

Anthu ambiri ankadziwa zoti Luis amatumikira Mulungu mokhulupirika. Mu 1994, nyuzipepala ina ya m’dzikoli inati: “Aliyense m’tauni ya San Cristobal amadziwa kuti Bambo Luis Eduardo Montás ndi munthu wabwino kwambiri. Kunena zoona, ndi dalitso kukhala ndi munthu wotere. Amaganizira anthu ndipo ndi wodekha. Anthu m’tauni yonseyi amadziwa kuti bambowa ndi Mkhristu weniweni.”