Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 DOMINICAN REPUBLIC

Yehova Watsegula Mitima ya Anthu Ambiri

Leonardo Amor

Yehova Watsegula Mitima ya Anthu Ambiri
  • KUBADWA 1943

  • KUBATIZIDWA 1961

  • MBIRI YAKE Anaphunzira Baibulo ali kamnyamata ndipo wakhala mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zoposa 50.

Ndinabatizidwa mu 1961, patangopita mwezi umodzi kuchokera pamene Trujillo anaphedwa. Pa nthawiyo ndinkaphunzira uloya ku yunivesite. Bambo anga ankafuna kuti ndidzakhale loya koma ine ndinaona kuti maphunziro a Yehova ndi apamwamba kuposa uloyawo. Ndiyeno ndinasiya sukulu ku yunivesiteko koma bambo anga sanasangalale nazo. Pasanapite nthawi ndinayamba kuchita upainiya wapadera.

Pa nthawi ina ndinatumizidwa kumzinda wa La Vega. Mumzindawu chikatolika chinali chitazika mizu kwambiri. Nthawi yonse imene ndinakhala kumeneko palibe amene ankafuna kuphunzira. Ndinkakamba nkhani za onse koma amene ankapezekapo ndi munthu m’modzi amene ndinkachita naye upainiya. Koma Yehova anandithandiza chifukwa choti ndinkakonda kuphunzira Baibulo pandekha, kupezeka pamisonkhano ikuluikulu ndiponso kupemphera kuchokera pansi pa mtima.  Ndinkapempha Yehova kuti athandize n’cholinga choti mumzindawu mukhale mpingo. Panopa ndimasangalala kwambiri chifukwa kuli Nyumba za Ufumu 6, mipingo 14 ndiponso ofalitsa oposa 800.

Mu 1965 ndinakwatira Ángela ndipo mu 1981 tinaitanidwa ku Beteli. Pamene ndinkabatizidwa, m’dzikoli munali ofalitsa 681 okha koma pano kuli ofalitsa oposa 36,000. Anthu masauzande ambiri amapezeka pa misonkhano ikuluikulu. Ndikaganizira mmene zinalili m’mbuyomu ndimasangalala kwambiri poona kuti Yehova watsegula mitima ya anthu ambiri kuti amve uthenga wa m’Baibulo.

Komiti ya Nthambi. Kuchokera kumanzere: Reiner Thompson, Juan Crispín, Thomas Dean, Leonel Peguero, Leonardo Amor ndi Richard Stoddard