Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 114: Mapeto a Kuipa Konse

Nkhani 114: Mapeto a Kuipa Konse

KODI mukuonanji pano? Inde, gulu la nkhondo lokwera pa akavalo oyera. Koma onani kumene iwo akuchokera. Akavalo’wo akuthamanga kuchokera kumwamba m’mitambo! Kodi kumwamba kuli akavalo eni-eni?

Yesu ndi Mfumu kumwamba

Ai, awa si akavalo eni-eni. Tikudziwa izi chifukwa chakuti akavalo sangathamange m’mitambo. Kodi si choncho? Koma Baibulo limanena za akavalo a kumwamba. Kodi mukudziwa chifukwa chake limatero?

N’chifukwa chakuti pa nthawi ina akavalo anagwiritsiridwa ntchito m’kumenya nkhondo. Chotero Baibulo limasimba za anthu kukhala akukwera pa akavalo akutsika kuchokera kumwamba kusonyeza kuti Mulungu ali ndi nkhondo yoti amenyane ndi anthu pa dziko lapansi. Kodi mukudziwa chimene malo a nkhondo’yi akuchedwa? Armagedo. Nkhondo imene’yo iyenera kuthetsa kuipa konse pa dziko lapansi.

Yesu ndiye adzatsogolera m’kumenya nkhondo’yi pa Armagedo. Pajatu, Yesu ndiye amene Yehova anam’sankha kukhala mfumu ya boma Lake. Ndicho chifukwa chake Yesu wabvala chisoti chachifumu. Ndipo lupanga’lo limasonyeza kuti iye adzapha adani a Mulungu onse. Kodi tiyenera kudabwitsidwa kuti Mulungu adaononga anthu onse.

Bwererani ku Nkhani 10. Kodi mukuonapo chiani? Inde, Chigumula chachikulu chimene chinaononga anthu oipa. Kodi ndani amene anachititsa Chigumula chimene’cho. Yehova Mulungu. Tsopano onani Nkhani 15. Kodi n’chiani chimene chikuchitika pano? Sodomu ndi Gomora akuonongedwa ndi moto umene Yehova akutumiza.

Tembenukirani ku Nkhani 33. Onani chimene chikuchitikira akavalo ankhondo’wo ndi magaleta a Aigupto. Kodi ndani amene anachititsa madzi’wo kuwaphimba. Yehova. Iye anakuchita kutetezera anthu ake. Onani Nkhani 76. Mudzaonamo kuti Yehova analola’di anthu ake Aisrayeli, kuonongedwa chifukwa cha kuipa kwao.

Tsono, sitiyenera kudabwa kuti Yehova adzatumiza magulu ake ankhondo kudzathetsa kuipa konse pa dziko lapansi. Koma taganizirani chimene zimene’zo zidzatanthauza! Tembenukirani kutseri’ku tione.

Chivumbulutso 16:16; 19:11-16.Mafunso

  • N’chifukwa chiyani Baibulo limanena za akavalo ali kumwamba?
  • Kodi dzina la nkhondo imene Mulungu adzamenye ndi anthu oipa padziko lapansi ndi chiyani, ndipo cholinga cha nkhondo imeneyi n’chiyani?
  • Kuchokera pachithunzipa, kodi Amene adzatsogolere pomenya nkhondoyo ndi ndani, n’chifukwa chiyani wavala chisoti chachifumu, ndipo kodi lupanga lake likutanthauza chiyani?
  • Tikakumbukira Nkhani 1015, ndi 33, n’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa kuti Mulungu adzawononga anthu oipa?
  • Kodi Nkhani 36 ndi 76 zikutisonyeza bwanji kuti Mulungu adzawononga anthu oipa ngakhale azinena kuti amalambira iyeyo?

Mafunso ena