Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 105: Akuyembekezera M’Yerusalemu

Nkhani 105: Akuyembekezera M’Yerusalemu

ANTHU ali pano’wa ndi atsatiri a Yesu. Amumvera nakhala m’Yerusalemu. Ndipo akali chiyembekezerere onse pamodzi, phokoso likudzaza nyumba’yo. Likumveka ngati chimphepo champhamvu. Ndiyeno malirime a moto akuonekera pa mitu pa ali yense wa ophunzira’wo. Kodi mukuona moto’wo pa ali yense wa iwo? Kodi zonse’zi zikutanthauzanji?

Akhristu oyambirira atalandira mzimu woyera

N’chozizwitsa! Yesu wabwerera kumwamba ali ndi Atate wake, ndipo akutsanulira mzimu woyera pa atsatiri ake. Kodi mukudziwa chimene mzimu’wu ukuwachititsa kuchita? Onse akuyamba kulankhula zinenero zosiyana-siyana.

Anthu ambiri m’Yerusalemu akumva phokoso limene likumveka ngati chimphepo champhamvu, nadza kudzaona chimene chikuchitika. Ena ali anthu ochokera ku mitundu ina amene adza kuno kaamba ka phwando la Aisrayeli la Pentekoste. N’zodabwitsa zotani zimene alendo’wa akulandira! Akumva ophunzira’wo akulankhula m’chinenero cha kwao ponena za zodabwitsa zimene Mulungu wachita.

Alendo’wo akuti: ‘Anthu’wa onse ngochokera ku Galileya. Nangano, ndi motani m’mene kuliri, kuti akukhoza kulankhula zinenero zosiyana-siyana’zi za kumaiko a kumene tachokera?’

Petro tsopano akuimirira nawalongosolera. Akukweza mau ake nauza anthu’wo m’mene Yesu anaphedwera ndi kuti Yehova anamuukitsa. Petro akuti: ‘Tsopano Yesu ali kumwamba ku dzanja lamanja la Mulungu. Ndipo watsanulira mzimu woyera wolonjezedwa’wo. N’chifukwa chake mwaona ndi kumva zozizwitsa’zi.’

Ndiyeno, Petro atanena zinthu’zi, ambiri akumva chisoni kwambiri ndi zimene zinachitidwira Yesu. Iwo akufunsa kuti, ‘Tidzachita chiani?’ Petro akuwauza kuti: ‘Mufunikira kusintha miyoyo yanu ndi kubatizidwa.’ Chotero pa tsiku’lo anthu 3,000 anabatizidwa nakhala otsatira Yesu.

Machitidwe 2:1-47.Mafunso

  • Monga momwe chithunzichi chikusonyezera, n’chiyani chikuchitikira otsatira a Yesu amene akhala akuyembekezera m’Yerusalemu?
  • Kodi alendo amene abwera ku Yerusalemu akuona zodabwitsa zotani?
  • Kodi Petro akulongosolera anthuwo chiyani?
  • Kodi anthuwo akumva bwanji atamvetsera Petro, ndipo iye akuwauza kuti achite chiyani?
  • Kodi ndi anthu angati amene anabatizidwa tsiku limenelo pa Pentekoste wa m’chaka cha 33 Kristu Atabwera?

Mafunso ena