Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chigawo 7: Chiukiriro cha Yesu Mpaka pa Kumangidwa kwa Paulo

Chigawo 7: Chiukiriro cha Yesu Mpaka pa Kumangidwa kwa Paulo

Pa tsiku lachitatu pambuyo pa imfa yake, Yesu anaukitsidwa. Pa tsiku’lo iye anaonekera kwa atsatiri ake pa nthawi zisanu zosiyana-siyana. Yesu anapitirizabe kuonekera kwa iwo kwa masiku 40. Ndiyeno, ophunzira ake ali chipenyere, iye anakwera kumwamba. Masiku khumi pambuyo pake Mulungu anatsanulira mzimu woyera pa atsatiri a Yesu oyembekezera m’Yerusalemu’wo.

Kenako, adani a Mulungu anachititsa atumwi kuikidwa m’ndende, koma mngelo anawamasula. Wophunzira Stefano anaponyedwa miyala ndi otsutsa’wo mpaka kufa. Koma tikuphunzira m’mene Yesu anasankhira mmodzi wa otsutsa’wo kukhala mtumiki wake wapadera, ndipo anakhala mtumwi Paulo. Ndiyeno, patapita zaka zitatu ndi theka chiyambire pa imfa ya Yesu, Mulungu anatumiza mtumwi Petro kukalalikira Korneliyo wosakhala Myuda’yo ndi banja lake.

Pafupi-fupi zaka 13 pambuyo pake Paulo anayamba ulendo wake woyamba wolalikira. Pa ulendo wake wachiwiri Timoteo akutsagana ndi Paulo. Tikuphunzira m’mene Paulo ndi anzake oyenda nawo anakhalira ndi nthawi zosangalatsa m’kutumikira Mulungu. Potsirizira pake, Paulo anaikidwa m’ndende m’Roma. Zaka ziwiri pambuyo pake iye anamasulidwa, komano anaikidwa’nso m’ndende naphedwa. Zochitika za CHIGAWO 7 zinachitika m’kati mwa nyengo ya nthawi ya zaka 32.

Sauli anachita khungu chifukwa cha kuwala