Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 99: M’chipinda Chapamwamba

Nkhani 99: M’chipinda Chapamwamba

TSOPANO ndi usiku wa Lachinai, masiku awiri pambuyo pake. Yesu ndi atumwi ake 12 adza m’chipinda chapamwamba chachikulu’chi kudzadya chakudya cha Paskha. Mwamuna amene mukumuona akuchoka’yo ndiye Yudasi Iskariote. Iye akumka kukauza ansembe m’mene angapezere Yesu.

Chakudya chamadzulo cha Ambuye

Patatsala tsiku limodzi kuti izi zichitike, iye akumka kwa iwo nawafunsa kuti: ‘Mudzandipatsanji ngati ndikuthandizani kugwira Yesu?’ Iwo akuti: ‘Ndalama za silva makumi atatu.’ Tsopano Yudasi akumka kukakumana ndi amuna’wa kuti awatsogolere kwa Yesu. Kodi izi si zoopsya?

Chakudya cha Paskha chatha. Yesu tsopano akuyamba chakudya china chapadera. Akupatsa atumwi ake mtanda wa mkate nati: ‘Idyani uwu, chifukwa uwu utanthauza thupi langa limene lidzaperekedwera inu.’ Ndiyeno akuwapatsa chikho cha vinyo nati: ‘Imwani, chifukwa uwu utanthauza mwazi wanga, umene uyenera kutsanulidwa kaamba ka inu.’ Baibulo limachicha ‘chakudya cha madzulo cha Ambuye,’ kapena ‘Mgonero wa Ambuye.’

Aisrayeli anadya Paskha kuwakumbutsa nthawi imene mngelo ‘anapitirira’ nyumba zao m’Igupto, napha ana oyamba kubadwa m’nyumba za Aigupto. Koma tsopano Yesu akufuna kuti atsatiri ake am’kumbukire, ndi m’mene anaperekera moyo wake kaamba ka iwo. Ndicho chifukwa chake iye akuwauza kukumbukira chakudya chapadera’chi chaka ndi chaka.

Atadya Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, akuuza atumwi ake kukhala olimba mtima ndi amphamvu m’chikhulupiriro. Potsirizira pake, akuyimba nyimbo kwa Mulungu nachoka. Ndi usiku kwambiri tsopano, kupitirira pang’ono pakati pa usiku. Tiyeni tione kumene akupita.

Mateyu 26:14-30; Luka 22:1-39; Yohane chaputala 13 mpaka 17; 1 Akorinto 11:20.Mafunso

  • Monga momwe asonyezera pachithunzipa, n’chifukwa chiyani Yesu ndi atumwi ake 12 ali m’chipinda chachikulu chapamwamba?
  • Kodi mwamuna akuchokayo ndi ndani, ndipo akukachita chiyani?
  • Kodi Yesu akuyambitsa chakudya chapadera chotani atatha kudya chakudya cha Paskha?
  • Paskha ankakumbutsa Aisrayeli za chiyani, ndipo chakudya chapadera chimenechi chimakumbutsa otsatira a Yesu za chiyani?
  • Chakudya Chamadzulo cha Ambuye chitatha, Yesu akuuza otsatira ake chiyani, ndipo iwo akuchita chiyani?

Mafunso ena