Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 90: Ndi Mkazi pa Chitsime

Nkhani 90: Ndi Mkazi pa Chitsime

YESU anaima kuti apumule pafupi ndi chitsime m’Samariya. Ophunzira ake anali atalowa m’mudzi kukagula chakudya. Mkazi amene Yesu akulankhula nayeyo wadza kudzatunga madzi. Akuti: ‘Ndipatse madzi ndimwe.’

Yesu akulankhula ndi mkazi wachisamariya

Izi zikudabwitsa mkazi’yo kwambiri. Kodi mukudziwa chifukwa chake? N’chifukwa chakuti Yesu ndi Myuda, ndipo iye ndi Msamariya. Ndipo Ayuda ochuluka samakonda Asamariya. Sangalankhule nawo! Koma Yesu amakonda anthu a mitundu yonse. Chotero akuti: ‘Ukadadziwa amene akukupempha madzi, ukadam’pempha ndipo akadakupatsa madzi opatsa moyo.’

‘Mbuyanga,’ akutero mkazi’yo, chitsime’chi n’chakuya, ndipo mulibe chotungira. Kodi mukawatenga kuti madzi opatsa moyo’wa?’

‘Ngati umwa madzi a m’chitsime’chi udzamva’nso ludzu,’ analongosola motero Yesu. ‘Koma madzi amene ndidzapereka angakhalitse munthu ndi moyo kosatha.’

‘Mbuyanga,’ akutero mkazi, ‘ndipatseni madzi’wa! Pamenepo sindidzamva’nso ludzu. Ndipo sindizafunikira’nso kudza kuno kudzatunga madzi.’

Mkazi’yo akuganiza kuti Yesu akunena madzi eni-eni. Koma iye akunena za choonadi chonena za Mulungu ndi ufumu wake. Choondi’chi chiri ngati madzi opatsa moyo. Chingapatse munthu moyo wosatha.

Yesu tsopano akuuza mkazi’yo kuti: ‘Pita ukaitane mwamunako nubwere’nso.’

Iye akuyankha kuti, ‘Ndiribe mwamuna.’

‘Wayankha bwino,’ akutero Yesu. ‘Koma wakhala ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene uli naye tsopano si mwamuna wako.’

Mkazi’yo akudabwa, chifukwa chakuti zonse’zi n’zoona. Kodi Yesu anadziwa bwanji zinthu zonse’zi? Inde, chifukwa chakuti Yesu ndiye Wolonjezedwa’yo wotumizidwa ndi Mulungu, ndipo Mulungu amam’patsa chidziwitso’chi. Pa nthawi ino ophunzira a Yesu akubwera, ndipo akudabwa kuti iye akulankhula ndi mkazi Wachisamariya.

Kodi m’zonse’zi tikuphunziramo chiani? Zikusonyeza kuti Yesu ali wokoma mtima kwa anthu a mafuko onse. Ife’nso tiyenera kutero. Sitiyenera kuganiza kuti anthu ena ngoipa chifukwa chabe chakuti iwo ndi pfuko lina. Yesu amafuna kuti anthu onse adziwe choonadi chimene chimatsogolera ku moyo wamuyaya. Ndipo nafe’nso tiyenera kufuna kuthandiza anthu kuphunzira choonadi.

Yohane 4:5-43; 17:3.Mafunso

  • N’chifukwa chiyani Yesu waima pachitsime m’Samariya, ndipo akunena chiyani kwa mkazi pamenepo?
  • N’chifukwa chiyani mkaziyo akudabwa, kodi Yesu akumuuza chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani akumuuza zimenezi?
  • Kodi mkaziyo akuganiza kuti Yesu akunena za madzi otani, koma kodi Yesu akutanthauza madzi otani?
  • N’chifukwa chiyani mkaziyo akudabwa poona zimene Yesu akudziŵa za iye, ndipo kodi anazidziŵa bwanji?
  • Kodi tingaphunzire maphunziro otani pa nkhani ya mkazi pachitsime?

Mafunso ena