Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 85: Yesu Abadwira M’khola

Nkhani 85: Yesu Abadwira M’khola

KODI mukudziwa kakhanda’ka? Inde, ndiko Yesu. Wangobadwa kumene m’khola. Khola ndiro kumene zifuyo zimasungidwa. Mariya wagoneka Yesu modyera ng’ombe, amene ali malo m’mene mumasungidwira zakudya za aburu ndi zifuyo zina. Koma kodi n’chifukwa ninji iye ndi Yosefe ali muno limodzi ndi zinyama’zi? Awa sindiwo malo obadwira mwana kodi si choncho?

Ai, sindiwo. Koma nachi chifukwa chake ali muno: Wolamulira wa Roma, Kaisara Augusto, anapanga lamulo lakuti ali yense ayenera kubwerera ku mzinda umene iye anabadwira kukalembetsa dzina lake m’kaundula. Eya, Yosefe anabadwira muno m’Betelehemu. Koma pofika iye ndi Mariya, panalibe malo pali ponse kaamba ka iwo. Chotero iwo ayenera kudzakhala muno ndi zinyama’zi. Ndipo pa tsiku lomwe’li Mariya akubala Yesu! Koma, monga momwe mukuonera, ali bwino.

Yosefe, Mariya ndi Yesu ali wakhanda

Kodi mukuona abusa’wo akudza kudzaona Yesu? Iwo anali kubusa usiku akuyang’anira nkhosa zao, ndipo kuunika kunawawalira. Anali mngelo! Abusa’wo anaopa kwambiri. Koma mngelo’yo anati: ‘Musaope! Ndakutengerani mbiri yabwino. Lero lino, m’Betelehemu, Kristu Ambuye anabadwa. Iye adzapulumutsa anthu! Mudzam’peza atakulungidwa mu msalu atagona modyera ng’ombe.’ Mwadzidzidzi angelo ambiri akudza nayamba kutamanda Mulungu. Chotero pa nthawi yomweyo abusa’wa akufulumira kukaona Yesu, ndipo tsopano am’peza.

Kodi mukudziwa chifukwa chake Yesu ali wapadera kwambiri? Kodi mukudziwa amene iye ali kweni-kweni? Pajatu, m’nkhani yoyambirira ya bukhu’li tinalongosola za Mwana woyamba wa Mulungu. Mwana’yu anagwira ntchito limodzi ndi Yehova m’kulenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi chinthu china chiri chonse. Eya, amene’yu ndiye Yesu’yo!

Inde, Yehova anatenga moyo wa Mwana wake kuuchotsa kumwamba nauika m’mimba mwa Mariya. Pomwepo mwana anayamba kukula m’mimba mwakemo monga momwe’di ana ena amakulira m’mimba mwa amao. Koma mwana uyu anali Mwana wa Mulungu. Potsirizira pake Yesu anabadwa muno m’khola la m’Betelehemu. Kodi mukuona tsopano chifukwa chake angelo’wo anali achimwemwe kwambiri kukhala okhoza kunena zakuti Yesu anali atabadwa?

Luka 2:1-20.Mafunso

  • Kodi khanda lili pachithunzili ndi ndani, ndipo kodi Mariya akuligoneka kuti?
  • N’chifukwa chiyani Yesu anabadwira m’khola limodzi ndi zifuyo?
  • M’chithunzichi, kodi amuna amene akuloŵa m’kholawo ndi ndani, ndipo kodi mngelo anawauza chiyani?
  • N’chifukwa chiyani Yesu ali wapadera kwambiri?
  • N’chifukwa chiyani Yesu angatchedwe Mwana wa Mulungu?

Mafunso ena