Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 100: Yesu M’munda

Nkhani 100: Yesu M’munda

ATACHOKA m’chipinda chapamwamba’cho, Yesu ndi atumwi ake akumka ku munda wa Getsemane. Iwo akhala akudza kuno nthawi zambiri. Yesu akuwauza kukhala maso ndi kupemphera. Ndiyeno akumka cha apo, nawerama pansi napemphera.

Kenako Yesu akudza kumene kuli atumwi ake. Kodi muganiza akuchitanji? Ali mtulo! Katatu Yesu akuwauza kuti ayenera kukhala maso, koma nthawi iri yonse imene akubwerera akuwapeza ali mtulo. ‘Kodi mungagone bwanji pa nthawi yonga ino?’ akutero Yesu pa nthawi yotsiriza imene iye akubwerera. ‘Nthawi yakwana yakuti ndiperekedwe kwa adani anga.’

Pa nthawi yomwe’yo phokoso la khamu lalikulu likumveka. Onani! Amuna’wo akudza ndi malupanga ndi zibonga! Ndipo anyamula nyali zowaunikira. Pofika pafupi, wina akutuluka m’khamu’lo nadza kwa Yesu. Akumpsyomsyona, monga momwe mukuonera pano. Munthu’yu ndiye Yudasi Isikariote! Kodi akupsompsyoneranji Yesu?

Yudasi akumupereka Yesu

Yesu akum’funsa kuti: ‘Yudasi, kodi ukundipereka mwa kupsyompsyona? Inde, kupsyompsyona’ko ndiko chizindikiro. Kukudziwitsa amuna’wo kuti uyu ndiye Yesu, munthu amene iwo akufuna. Chotero adani’wo akudza nam’gwira. Koma Petro sakuwalola kutenga Yesu popanda nkhondo. Iye akusolola lupanga limene wadza nalo nakantha nalo munthu wokhala chifupi naye. Lupanga’lo langophonya mutu wa munthu’yo nalingodula khutu lakumanja. Koma Yesu akukhudza khutu la munthu’yo nalichiza.

Yesu akuuza Petro kuti: ‘Bwezera lupanga lako m’chimake. Kodi suganiza kuti ndingapemphe Atate wanga zikwi za angelo kudzandipulumutsa?’ Inde, angathe! Koma iye sakupempha Mulungu kutumiza angelo ali onse, chifukwa iye akudziwa kuti nthawi yakwana yakuti adani ake am’gwire. Chotero akuwalola kum’tenga. Tiyeni tione zimene zikuchitikira Yesu tsopano.

Mateyu 26:36-56; Luka 22:39-53; Yohane 18:1-12.Mafunso

  • Kodi Yesu ndi ophunzira ake akupita kuti atachoka m’chipinda chapamwamba, ndipo kodi akuwauza kuti achite chiyani?
  • Kodi Yesu akupeza chiyani atabwerera pamene pali atumwiwo, ndipo zimenezi zikuchitika kangati?
  • Ndani amene akuloŵa m’mundamo, ndipo Yudasi Isikariote akuchita chiyani, monga momwe asonyezera pachithunzipa?
  • N’chifukwa chiyani Yudasi akumpsopsona Yesu, ndipo Petro akuchita chiyani?
  • Kodi Yesu akunena chiyani kwa Petro, koma n’chifukwa chiyani Yesu sakupempha Mulungu kutumiza angelo?

Mafunso ena