Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 68: Anyamata Awiri Oukitsidwa

Nkhani 68: Anyamata Awiri Oukitsidwa

NGATI mutafa, kodi amanu akamva bwanji ngati mutaukitsidwa? Akakhala okondwa kwambiri! Koma kodi munthu wakufa angaukitsidwe? Kodi zinayamba zachitikapo?

Taonani munthu’yu, mkazi’yo ndi kamnyamata’ko. Mwamuna’yo ndiye mneneri Eliya. Mkazi’yo ndi mkazi wamasiye wa ku Zerefati, kamyamata’ko ndi mwana wake. Tsiku lina kakudwala. Iye akudwala moonjezereka-onjezereka nafa potsirizira pake. Ndiyeno Eliya akumuuza kuti: ‘Ndipatse mwana’yo.

Eliya ali ndi mkazi wamasiye ndi mwana wake wamwamuna amene anaukitsidwa

Eliya akutenga mwana wakufa’yp kumka naye m’chipinda cha pamwamba nam’goneka pa kama. Ndiyeno akupemphera kuti: ‘O Yehova, dzutsani mwana’yu.’ Mwana’yo akuyambano kupuma! Pompo Eliya akutsika naye nati kwa mkazi’yo: ‘Taona, mwana wako ali moyo!’ N’cho chifukwa chake mai’yo ali wachimwemwe kwambiri.

Mneneri wina wochuka wa Yehova akuchedwa Elisa. Akutumikira monga wothandiza wa Eliya. Koma m’kupita kwa nthawi Yehova akum’gwiritsira ntchito kuchita zozizwitsa. Tsiku lina Elisa akumka ku mzinda wa Sunemu, kumene mkazi wina akum’komera mtima kwambiri. Pambuyo pake mkazi’yu anabala mwana wamwamuna.

M’mawa wina, atakula mwana’yo, akumka kukagwira ntchito kumunda. Mwadzidzidzi mwana’yo akulira kuti: ‘Mutu wanga ukuwawa!’ Atapita kunyumba akufa. Ndi chisoni chotani m’mene mai wake analiri!’ Pompo akukaitana Elisa.

Pofika Elisa, akulowa m’chipinda muli mwana wakufa’yo. Akupemphera kwa Yehova, nagona pamwamba pake. Posakhalitsa thupi la mwana’yo likutentha, akuyetsemula kasanu ndi kawiri. Ndi okondwa chotani nanga m’mene aliri mai wake pamene akudza nam’peza ali moyo!

Anthu ochuluka afa. Izi zachititsa mabanja ndi mabwenzi ao kukhala achisoni kwambiri. Ife tiribe mphamvu yodzutsa akufa. Koma Yehova ali nayo. Kenako tidzaphunzira m’mene adzaukitsira anthu mamiliyoni ochuluka’wo.

1 Mafumu 17:8-24; 2 Mafumu 4:8-37.


Mafunso

  • Kodi anthu atatu amene ali m’chithunziŵa ndi ndani, ndipo n’chiyani chikuchitikira kamnyamatako?
  • Kodi Eliya akupempherera chiyani chokhudza kamnyamatako, ndipo n’chiyani chikuchitika kenako?
  • Kodi dzina la wothandiza wa Eliya ndi ndani?
  • N’chifukwa chiyani Elisa akuitanidwa kunyumba kwa mkazi wa ku Sunemu?
  • Kodi Elisa akuchita chiyani, ndipo n’chiyani chikuchitikira mwana wakufayo?
  • Kodi Yehova ali ndi mphamvu zotani, monga momwe zinaonekera mwa Eliya ndi Elisa?

Mafunso ena