Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 65: Ufumu Ukugawanika

Nkhani 65: Ufumu Ukugawanika

KODI mukudziwa chifuka chake mwamuna’yu akung’amba mwiinjiro wake? Yehova anamuuza kutero. Munthu’yu ndi mneneri wa Mulungu Ahiya. Kodi mukudziwa chimene mneneri ali? Ndiye munthu amene Mulungu amamuuziratu zimene zidzachitika.

Ahiya ndi Rehobowamu

Pano Ahiya akulankhula ndi Yerobiamu. Yerobiamu ndiye munthu wosiyiridwa ndi Solomo uyang’aniro wa ntchito yake ya kumanga. Pamene Ahiya akukumana naye pa njira, Ahiya akuchita chozizwitsa. Akubvula mwiinjiro watsopano umene wabvala n’kuung’amba zidutswa 12. Iye akuuza Yerobiamu kuti: ‘Dzitengere zidutswa 10.’ Kodi mukudziwa chifukwa chake Ahiya akum’patsa zidutswa 10?

Iye akulongosola kuti Yehova akachotsa ufumu kwa Solomo. Iye akuti akapereka mafuko khumi kwa Yerobiamu. Izi zikutanthauza kuti mafuko awiri okha akasiyiridwa Rehobiamu mwana wa Solomo kuwalamulira.

Solomo pakumva zimene Ahiya anauza Yerobiamu, akupsya mtima kwambiri. Iye akuyesa kupha Yerobiamu. Koma Yerobiamu akuthawira ku Igupto. Posapita nthawi Solomo akufa. Iye anakhala mfumu kwa zaka 40, komano mwana wake Rehobiamu akukhala mfumu. Ali ku Igupto’ko Yerobiamu akumva kuti Solomo wafa, chotero akubwerera ku Israyeli.

Rehobiamu si mfumu yabwino. Iye ali woipa mtima kwambiri kwa anthu’wo koposa atate wake Solomo. Yerobiamu ndi akuluakulu ena kumka kwa Mfumu Rehobiamu nam’pempha kukhala wabwinopo kwa anthu. Koma iye sakumvetsera. Zoonandi, iye akukhala woipa mtima moonjezereka koposa kale. Chotero anthu’wo akupanga Yerobiamu kukhala mfumu pa mafuko 10, koma mafuko awiri la Benjamini ndi Yuda likukhalabe ndi Rehobiamu monga mfumu yao.

Yerobiamu sakufuna kuti anthu ake adzimka ku Yerusalemu kukalambira pa kachisi wa Yehova. Chotero akupanga ana ang’ombe awiri a golidi nachititsa anthu a ufumu wa mafuko 10 kuwalambira. Posakhalitsa dziko’lo likudzazidwa upandu ndi chiwawa.

Muli’nso bvuto mu ufumu wa mafuko awiri’wo. Zosakwanira zaka zisanu Rehobiamu atakhala mfumu, mfumu ya Igupto ikudza kudzamenyana ndi Yerusalemu. Iye akutenga chuma chochuluka m’kachisi wa Yehova. Chotero pambuyo pa kanthawi chabe kachisi’yo sali’nso monga m’mene analiri pamene anamangidwa.

1 Mafumu 11:26-43; 12:1-33; 14:21-31.Mafunso

  • Kodi amuna aŵiri amene ali m’chithunziŵa mayina awo ndi ndani, ndipo kodi amunawo ndi ndani?
  • Kodi Ahiya akuchita chiyani ndi mwinjiro umene wavala, ndipo kodi zimenezo zikutanthauza chiyani?
  • Kodi Solomo akuyesera kumutani Yerobiamu?
  • N’chifukwa chiyani anthu akupanga Yerobiamu kukhala mfumu pa mafuko 10?
  • N’chifukwa chiyani Yerobiamu akupanga ana ang’ombe aŵiri agolidi, ndipo n’chiyani chikuchitikira dzikolo posakhalitsa?
  • Kodi n’chiyani chikuchitikira ufumu wa mafuko aŵiri ndi kachisi wa Yehova ku Yerusalemu?

Mafunso ena