Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 62: Bvuto M’banja la Davide

Nkhani 62: Bvuto M’banja la Davide

DAVID atayamba kulamulira m’Yerusalemu, Yehova akupatsa gulu lake lankhondo zipambano zambiri pa adani ao. Yehova analonjeza kupatsa Aisrayeli dziko la Kanani. Ndipo tsopano, mwa chithandizo chake, dziko lonse limene linalonjezedwa’lo likukhala lao.

Davide ndi wolamulira wabwino. Amakonda Yehova. Chotero chinthu choyamba chimene iye akuchita atagonjetsa Yerusalemu ndicho kutengera likasa la chipangano la Yehova kumene’ko. Iye akufuna kumanga kachisi woliikamo.

Davide atakalamba, akupanga cholakwa choipa. Iye amadziwa kuti n’kolakwa kutenga kanthu ka munthu wina. Koma madzulo ena, ali pa tsindwi la mphala yake, akuyang’ana pansi naona mkazi wokongola kwambiri. Dzina lake ndi Bateseba, ndipo mwamuna wake ndi mmodzi wa ankhondo ake wochedwa Uriya.

Davide akufuna Bateseba kwambiri kwakuti akumuitanitsa ku mphala yake. Mwamuna wake ali kunkhondo. Chabwino, akugona naye ndipo pambuyo pake akupeza kuti adzabala mwana. Davide ali wobvutika maganizo kwambiri ndipo akutumiza mau kwa mkulu wake wankhondo Yoabu kuti Uriya aikidwe pa mzera wapatsogolo ku nkhondo kumene iye adzaphedwa. Atafa Uriya, Davide akukwatira Bateseba.

Yehova wakwiyira kwambiri Davide. Chotero akutumiza mtumiki wake Natani kukamuuza za machimo ake. Mukuona Natani uyo akulankhula ndi Davide. Davide ali ndi chisoni kwambiri ndi zimene wachita, chotero Yehova sakum’pha. Koma Yehova akuti: ‘Chifukwa chakuti wachita zoipa’zi, udzakhala ndi mabvuto ochuluka m’banja lako.’ Ndipo ndi bvuto lotani nanga limene Davide anali nalo!

Natani akum’patsa Davide uphungu

Choyamba, mwana wa Bateseba akufa. Kenako mwana wachisamba wa Davide Amnoni akukhala yekha ndi mlongo wake Tamara nam’kakamiza kugona naye. Mwana wake Abisalomu ali wokwiya kwambiri kwakuti akupha Amnoni. Kenako, Abisalomu akupeza chiyanjo cha anthu ambiri, ndipo akudzipangitsa kukhala mfumu. Potsirizira pake, Davide akupambana nkhondo yomenyana ndi Abisalomu, amene akuphedwa. Inde, Davide ali ndi mabvuto ochuluka.

M’kati mwa zonse’zi, Bateseba akubala mwana wamwamuna wochedwa Solomo. Davide ali wokalamba ndi wodwala, mwana wake Adoniya akuyesa kudzipanga kukhala mfumu. Pamenepo Davide anauza wansembe wochedwa Zadoki kuthira mafuta pamutu pa Solomo kusonyeza kuti Solomo adzakhala mfumu. Posakhalitsa Davide akufa ali ndi zaka 70. Iye analamulira zaka 40, koma tsono Solomo ndiye mfumu ya Israyeli.

2 Samueli 6:1-15; 11:1-27; 1 Mafumu 1:1-48.Mafunso

  • Kodi pamapeto pake n’chiyani chikuchitikira dziko la Kanani ndi chithandizo cha Yehova?
  • Kodi n’chiyani chikuchitika madzulo enaake Davide ali pa tsindwi la mphala yake?
  • N’chifukwa chiyani Yehova wakwiyira kwambiri Davide?
  • M’chithunzichi, kodi Yehova akutumiza ndani kukauza Davide za machimo ake, ndipo kodi munthu ameneyo akunena kuti n’chiyani chidzachitikira Davide?
  • Kodi Davide akukhala ndi vuto lotani?
  • Pambuyo pa Davide, ndani akukhala mfumu ya Israyeli?

Mafunso ena