Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 45: Kuoloka Mtsinje wa Yordano

Nkhani 45: Kuoloka Mtsinje wa Yordano

TAONANI! Aisrayeli akuoloka Mtsinje wa Yordano! Koma kodi madzi ali kuti? Chifukwa mvula yochuluka imabvumba nthawi imene’yo ya chaka, mtsinje’wo unali wodzadza kwambiri mphindi zowerengeka zapita’zo. Koma tsopano madzi onse apita! Ndipo Aisrayeli akuoloka pouma monga momwe anachitira’di pa Nyanja Yofiira! Kodi madzi onse anamka kuti? Tiyeni tione.

Aisiraeli akuwoloka Mtsinje wa Yorodano

Pamene inafika nthawi yoti Aisrayeli aoloke Mtsinje wa Yordano, nazi zimene Yehova anauza Yoswa kuuza anthu: ‘Ansembe ayenera kusenza likasa la chipangano ndi kutsogolera ife. Pamene iwo athibika mapazi ao m’madzi a Mtsinje wa Yordano, pamenepo madzi’wo adzaleka kuyenda.’

Chotero ansembe akusenza likasa la chipangano, nayenda nalo patsogolo pa anthu. Pofika ku Yordano, ansembe’wo akulowa m’madzimo. Iwo akuthamanga kwambiri ndipo ngwozama. Koma pamene mapazi ao angokhudza madzi’wo, akuyamba kuleka kuyenda! N’chozizwitsa! Yehova wasonkhanitsa pamodzi madzi kumtunda’ko. Chotero, posapita nthawi mulibe’nso madzi mu mutsinje’wo!

Ansembe onyamula likasa’wo akumka pakati pa mtsinje wouma’wo. Kodi mukuwaona m’chithunzi’cho? Ataima pamenepo, Aisrayeli onse akuyenda kuoloka Mtsinje wa Yordano pouma!

Ali yense ataoloka, Yehova akuuza Yoswa kuuza amuna amphamvu 12 kuti: ‘Lowani mu mtsinje kumene kwaima ansembe onyamula likasa’wo. Tolani miyala 12, ndi kuiimika pamene inu nonse mudzagona. Ndiyeno, m’tsogolo, akakufunsani ana anu chimene miyala’yi imatanthauza, muziwauza kuti madzi anaima pamene likasa la Yehova linaoloka Yordano. Miyala’yi idzakukumbutsani za chozizwitsa’chi!’ Yoswa akuimika’nso miyala 12 pamene panaima ansembe m’mbali mwa mtsinje’wo.

Yoswa

Pomaliza Yoswa akuuza ansembe osenza likasa kuti: ‘Tulukani m’Yordano.’ Atangotuluka, mtsinje’wo ukuyamba’nso kuyenda.

Yoswa 3:1-17; 4:1-18.Mafunso

 • Kodi Yehova akuchita chozizwitsa chotani kuti Aisrayeli awoloke mtsinje wa Yordano?
 • Kodi Aisrayeli ayenera kuchita chiyani chofunika chikhulupiriro kuti athe kuwoloka mtsinje wa Yordano?
 • N’chifukwa chiyani Yehova akuuza Yoswa kusonkhanitsa miyala 12 ikuluikulu kuchokera m’mphepete mwa mtsinjewo?
 • Kodi chikuchitika n’chiyani ansembe atangotuluka mu Yordano?

Mafunso ena

 • Ŵerengani Yoswa 3:1-17.

  Monga momwe nkhani imeneyi ikusonyezera, kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Yehova atithandize ndi kutidalitsa? (Yos. 3:1315; Miy. 3:5; Yak. 2:2226)

  Kodi mtsinje wa Yordano unkaoneka bwanji pamene Aisrayeli anawoloka kupita ku Dziko Lolonjezedwa, ndipo zimenezi zinalemekeza bwanji dzina la Yehova? (Yos. 3:15; 4:18; Sal. 66:5-7)

 • Ŵerengani Yoswa 4:1-18.

  Kodi miyala 12 imene anaitenga mu mtsinje wa Yordano n’kuiika ku Giligala inali ndi ntchito yanji? (Yos. 4:4-7)