Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 41: Njoka Yamkuwa

Nkhani 41: Njoka Yamkuwa
Mose ndi njoka yamkuwa

KODI ikuoneka ngati njoka yeni-yeni yozengenezedwa pa mtengo’yo? Ai. Njoka’yi ndi yamkuwa. Yehova anauza Mose kuiika pa mtengo kuti anthu aiyang’ane ndi kukhala ndi moyo. Koma njoka zina ziri pansi’zo n’zeni-zeni. Izo zaluma anthu ndi kuwadwalitsa. Kodi mukudziwa chifukwa chake?

N’chifukwa chakuti Aisrayeli alankhula motsutsa Mulungu ndi Mose. Iwo akudandaula kuti: ‘Munatitulutsiranji mu Igupto kuti tidzafere m’chipululu muno? Mulibe chakudya kapena madzi muno. Ndipo talema nako kudya mana.’

Koma mana n’chakudya chabwino. Mozizwitsa Yehova anawapereka kwa iwo. Ndipo mozizwitsa anawapatsa’no madzi. Koma anthu’wo sali othokoza kaamba ka m’mene Mulungu wawasamalirira. Chotero Yehova akutumiza njoka za ululu’zi kukawalanga. Njoka’zo zikuwaluma, nafa ambiri a iwo.

Aiisraeli akulumidwa ndi njoka

Kenako anthu’wo akudza kwa Mose nati: ‘Tachimwa, popeza tanena motsutsana ndi Yehova ndi inu. Tsopano pempherani kwa Yehova kuti atichotsere njoka’zi.’

Chotero Mose akupempherera anthu’wo. Ndipo Yehova akuuza Mose kupanga njoka yamkuwa iyi. Akumuuza kuiika pa mtengo, ndi kuti onse olumwa aiyang’ane. Mose akuchita zimene Mulungu akumuuza. Ndipo anthu olumwa’wo akuyang’ana pa njoka’yo nachira.

Muli phunziro lophunziridwa muno. Tonsefe, m’njira ina, tiri ngati Aisrayeli’wo amene analumidwa ndi njoka’zo. Tonsefe tiri mu mkhalidwe wakufa. Unguza-unguzani, ndipo mudzaona kuti anthu akukalamba, kudwala, ndi kufa. Izi ziri chifukwa chakuti mwamuna ndi mkazi oyamba, Adamu ndi Hava, anapandukira Yehova, ndipo ife tonse ana aofe, tinatero. Koma Yehova wapanga njira yoti tikhalire ndi moyo kosatha.

Yehova anatumiza Mwanake, Yesu Kristu, ku dziko lapansi. Yesu anapachikidwa pa mtengo chifukwa chakuti ambiri anam’ganizira kukhala woipa. Koma Yehova anapereka Yesu kwa ife. Ngati tiyang’ana kwa iye, ngati tim’tsatira, pamenepo tingakhale ndi moyo wosatha. Koma tidzaphunzira zina ponena za izi pambuyo pake.

Numeri 21:4-9; Yohane 3:14, 15.Mafunso

  • M’chithunzichi, kodi n’chiyani chimene achikulungiza pamtengocho, ndipo n’chifukwa chiyani Yehova anauza Mose kuti achiike pamenepo?
  • Kodi anthuwo akusonyeza bwanji kuti sakuthokoza chifukwa cha zinthu zonse zimene Mulungu wawachitira?
  • Kodi anthuwo akupempha Mose kuchita chiyani Yehova atawatumizira njoka za ululu powalanga?
  • N’chifukwa chiyani Yehova akuuza Mose kuti apange njoka yamkuwa?
  • Kodi tingaphunzirepo chiyani pa nkhani imeneyi?

Mafunso ena