Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 29: Chifukwa Chake Mose Akuthawa

Nkhani 29: Chifukwa Chake Mose Akuthawa

MUKUONA Mose’yo akuthawa m’Igupto. Mukuona amuna’wo akum’thamangitsa? Kodi mukudziwa chifukwa chake akufuna kupha Mose? Tiyeni tione ngati tingathe.

Mose akuthawa ku Iguputo

Mose anakulira m’nyumba ya Farao, wolamulira wa Igupto. Iye anakhala munthu wanzeru ndi wamphamvu kwambiri. Iye anadziwa kuti sanali Muigupto, koma kuti makolo ake eni-eni anali Aisrayeli.

Tsiku lina, ali ndi zaka 40, Mose analingalira kupita kukaona m’mene mtundu wake unaliri. Kuchitiridwa kwao kunali koopsya. Iye anaona Muigupto akumenya kapolo Wachiisrayeli. Mose anaunguza-unguza, ndipo posaona ali yense, anakantha Muigupto, nafa. Pompo Mose anakwirira mtembo wake mu mchenga.

M’mawa mwake Mose anakaona’nso anthu ake. Iye anaganiza kuti akawathandiza kuti asakhale’nso akapolo. Koma anaona Aisrayeli awiri akumenyana, nati iye kwa wolakwa’yo: ‘Kodi umenyeranji mbale wako?’

Munthu’yo anati: ‘Wakuika ndani kukhala wolamulira ndi woweruza wathu? Kodi ufuna undiphe monga muja unaphera Muigupto uja?’

Mose tsopano anaopa. Anadziwa kuti anthu adziwa zimene iye anachitira Muigupto. Ngakhale Farao anazimva, natumiza anthu kukapha Mose. Ndicho chifukwa chake Mose anafunikira kuthawa mu Igupto.

Mose atachoka mu Igupto, anamka kutali ku Midyani. Kumene’ko anakumana ndi banja la Yetero, nakwatira mwana wake wamkazi mmodzi wochedwa Zipora. Mose anakhala mbusa wa nkhosa woweta nkhosa za Yetero. Kwa zaka 40 iye anakhala m’Midyani. Tsopano anali ndi zaka 80. Tsiku lina, akuyang’anira nkhosa za Yetero, chozizwitsa chinachitika chimene chinasintha moyo wonse wa Mose. Tiyeni tione kuti chozizwitsa chimenechi chinali chotani.

Ekisodo 2:11-25; Machitidwe 7:22-29.Mafunso

  • Kodi Mose anakulira kuti, koma kodi anadziŵa chiyani za makolo ake?
  • Kodi Mose ali ndi zaka 40 anachita chiyani?
  • Kodi Mose ananena chiyani kwa mwamuna wachiisrayeli amene ankamenya mnzake, ndipo kodi mwamunayo anayankha kuti chiyani?
  • N’chifukwa chiyani Mose anathawa ku Igupto?
  • Kodi Mose anathaŵira kuti, ndipo kodi kumeneko anakumana ndi ndani?
  • Kodi Mose anachita chiyani kwa zaka 40 atathaŵa ku Igupto?

Mafunso ena