Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 26: Yobu Akhulupirira Mulungu

Nkhani 26: Yobu Akhulupirira Mulungu

KODI mukumvera chisoni munthu wodwala’yu? Dzina lake ndi Yobu, ndipo mkazi’yo ndi mkazi wake. Kodi mukudziwa zimene akuuza Yobu? ‘Tukwana Mulungu ufe.’ Tiyeni tione chifukwa chake akanena zotero’zo, ndi chifukwa chake Yobu anabvutika kwambiri.

Yobu atatuluka zilonda

Yobu anali munthu wokhulupirika womvera Yehova. Anakhala m’dziko la Uzi, pafupi ndi Kanani. Yehova anam’konda kwambiri, koma panali wina amene anam’da. Kodi mukum’dziwa?

Ndiye Satana. Pajatu, Satana ndiye mngelo woipa amene amada Yehova. Iye anachititsa Adamu ndi Hava kusamvera Yehova, ndipo anaganiza kuti akachititsa ali yense kusamvera’nso Yehova. Koma kodi anali wokhoza? Ai. Tangoganizira za amuna ndi akazi okhulupirika ochuluka’wo amene timaphunzira za iwo. Kodi mungachule angati?

Yakobo ndi Yosefe atafa mu Igupto, Yobu anali munthu wokhulupirika kopambana kwa Yehova m’dziko lonse lapansi. Yehova anafuna kudziwitsa Satana kuti sakanatha kuchititsa ali yense kuipa, chotero anati: ‘Ona Yobu. Ona kundikhulupirira kwake.’

Satana anatsutsa nati, ‘Ali wokhulupirika, chifukwa mumam’dalitsa ndipo ali ndi zinthu zabwino. Koma mukam’chotsera izi, adzakunenerani mwano.’

Tsono, Yehova anati: ‘Pita. Kazichotse. Chita zoipa zonse zimene ufuna kwa Yobu. Tidzaona ngati adzanditukwana. Koma ona kuti sukumupha.’

Satana, choyamba anadezetsa akuba ndi kuba ng’ombe ndi ngamila za Yobu ndipo nkhosa zake zinaphedwa. Napha ana ake 10 mu mkuntho. Kenako, Satana anakantha Yobu ndi nthenda yoopsya. Yobu anabvutika kwambiri. N’chifukwa chake mkazi wake anati: ‘Tukwana Mulungu ufe.’ Koma iye anakana. Ndipo’nso, anadza mabwenzi atatu namuuza kuti anachita zoipa. Koma Yobu anakhalabe wokhulupirika.

Izi zinakondweretsa’di Yehova, nadalitsa Yobu monga m’chithunzi’chi. Anachiritsa nthenda yake. Nakhala ndi ana ena 10, ndi ng’ombe, nkhosa ndi ngamila zowirikiza zakale.

Kodi mudzakhulupirika kwa Yehova ngati Yobu? Mukatero, iye adzakudalitsani. Mudzakhoza kukhala ndi moyo kosatha dziko lonse litakongoletsedwa ngati munda wa Edene.

Yobu 1:1-22; 2:1-13; 42:10-17.

Yobu ndi banja lake


Mafunso

  • Kodi Yobu anali ndani?
  • Kodi Satana anayesera kuchita chiyani, koma kodi anapambana?
  • N’chiyani chimene Yehova analoleza Satana kuchita, ndipo n’chifukwa chiyani anamuloleza kuchita zimenezo?
  • N’chifukwa chiyani mkazi wa Yobu anamuuza kuti ‘tukwana Mulungu ufe’? (Onani chithunzi.)
  • Monga mukuonera pa chithunzi chachiŵiricho, kodi Yehova anadalitsa bwanji Yobu, ndipo anamudalitsa chifukwa chiyani?
  • Ngati ifeyo, mofanana ndi Yobu, tikhala okhulupirika kwa Yehova, kodi tidzalandira madalitso otani?

Mafunso ena