Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 22: Yosefe Aikidwa M’ndende

Nkhani 22: Yosefe Aikidwa M’ndende

YOSEFE ali ndi zaka 17 zokha pamene akutengeredwa ku Igupto. Kumene’ko akugulitsidwa kwa Potifara. Potifara amagwirira ntchito mfumu ya Igupto, yochedwa Farao.

Yosefe ali m’ndende

Yosefe akugwirira ntchito zolimba mbuyake. Potifara. Tsono posinkhuka Yosefe, Potifara akumuika kukhala woyang’anira wa banja lake lonse. Nanga, n’chifukwa ninji, Yosefe ali m’ndende muno? N’chifukwa cha mkazi wa Potifara.

Yosefe akukhala mnyamata wokongola, ndipo mkazi wa Potifara akufuna kugona naye. Koma Yosefe akudziwa izi kukhala zoipa, ndipo sangazichite. Mkazi’yo akupsya mtima kwambiri. Chotero pofika mwamuna wake akum’namiza kuti: ‘Yosefe woipa uja anandinyenga kuti agone nane!’ Iye akukhulupirira mkazi wake, ndipo wam’psyera mtima kwambiri Yosefe. Chotero akum’chititsa kumangidwa.

Wosunga ndende posapita nthawi akuona kuti iye ndi munthu wabwino. Chotero akumuika pa uyang’aniro wa akaidi ena onse. Kenako Farao akukwiyira woperekera zakumwa ndi wophika yemwe, nawaika mu ndende. Usiku wina yense wa iwo akulota loto lapadera, koma sakudziwa tanthauzo la maloto ao. M’mawa mwake Yosefe akuti: ‘Ndiuzeni maloto anu.’ Atamuuza, mwa chithandizo cha Mulungu, iye akulongosola tanthauzo la maloto ao.

Woperekera zakumwa’yo, anauzidwa kuti: ‘M’masiku atatu udzamasulidwa, nudzakhala woperekera zakumwa wa Farao kachiwiri’nso.’ Yosefe akuti’nso: ‘Utatuluka, kauze Farao za ine, ndi kundithandiza kutuluka muno.’ Koma kwa wophika’yo, akuti: ‘M’masiku atatu Faro adzakudula mutu.’

M’masiku atatu zinachitika’di. Farao anadula mutu wa wophika. Koma, woperekera zakumwa’yo akumasulidwa nayamba kutumikira’nso mfumu. Koma akuiwala za Yosefe! Sakuuza Farao za iye ndipo Yosefe akukhalabe m’ndende.

Genesis 39:1-23; 40:1-23.Mafunso

  • Kodi Yosefe ali ndi zaka zingati pamene akupita naye ku Igupto ndipo n’chiyani chikuchitika pamene akufika kumeneko?
  • Kodi chachitika n’chiyani kuti Yosefe aikidwe m’ndende?
  • Kodi Yosefe akupatsidwa udindo wanji m’ndendemo?
  • Ali m’ndende, kodi Yosefe akuchitira chiyani woperekera zakumwa ndi wophika wa Farao?
  • Kodi chikuchitika n’chiyani woperekera zakumwayo atatuluka m’ndende?

Mafunso ena