Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 9: Nowa Akhoma Chingalawa

Nkhani 9: Nowa Akhoma Chingalawa
Anthu akumuseka Nowa

NOWA anali ndi mkazi ndi ana amuna atatu. Maina a ana’wo anali Semu, Hamu ndi Yafeti. Ali yense wa iwo anali ndi mkazi. Chotero munali anthu asanu ndi atatu m’banja la Nowa.

Mulungu tsopano anafuna kuti Nowa achite kanthu kachilendo. Anamuuza kukhoma chingalawa. Chingalawa’chi chinali ngati sitima, koma chinaoneka ngati chibokosi chachitali. ‘Uchipange cha zipinda zosanja zitatu,’ anatero Mulungu, ‘nupangemo zipinda.’ Zipinda zinali za Nowa ndi banja lake, zinyama ndi zakudya zao zofunika.

Mulungu anauza’nso Nowa kuchipanga kuti chisalowe madzi. Iye anati: ‘Ndidzadzetsa chigumula chachikulu ndi kuononga dziko lonse. Ali yense wosakhala m’chingalawa adzafa.’

Nowa ndi ana ake anamvera Yehova nayamba kukhoma’ko. Koma anthu ena ankangoseka. Anaipabe chiipire. Palibe aliyense anakhulupirira Nowa pamene anawauza zimene Mulungu adzachita.

Anthu am’banja la Nowa akulowetsa zakudya komanso zinyama m’chingalawa

Kunatenga nthawi yaitali kukhoma chingalawa’cho chifukwa chinali chachikulu kwambiri. Pambuyo pa zaka zambiri chinatha. Tsopano Mulungu anauza Nowa kulowetsamo zinyama. Anati alowetsemo ziwiri-ziwiri za mitundu ina, zazimuna ndi zazikazi zomwe. Koma mitundu ina, Mulungu anauza Nowa kulowetsamo zisanu ndi ziwiri. Mulungu anamuuza’nso kulowetsamo mitundu yonse ya mbalame. Nowa anachita’di zonenedwa ndi Mulungu’zo.

Kenako, Nowa ndi banja lake nawo’nso analowa m’chingalawa. Mulungu natseka chitseko. Alimo, Nowa ndi banja lake anayembekeza. Tayerekezerani muli m’chingalawa’cho, mukuyembekezera nawo. Kodi kudzakhala’di chigumula monga momwe ananenera Mulungu?

Genesis 6:9-22; 7:1-9.Mafunso

 • Kodi m’banja la Nowa munali anthu angati, ndipo mayina a ana ake aamuna atatu anali ndani?
 • Kodi ndi kanthu kachilendo kotani kamene Mulungu anapempha Nowa kuchita, ndipo anamupempha kuchita zimenezi chifukwa chiyani?
 • Kodi anthu okhala pafupi ndi Nowa anachita chiyani pamene anawauza za chingalawa?
 • Kodi Mulungu anauza Nowa kuti achite chiyani ndi zinyama?
 • Mulungu atatseka khomo la chingalawa, kodi Nowa ndi banja lake anafunika kuchita chiyani?

Mafunso ena

 • Ŵerengani Genesis 6:9-22.

  Kodi n’chiyani chinachititsa Nowa kukhala munthu wabwino kopambana wolambira Mulungu woona? (Gen. 6:922)

  Kodi Yehova amachiona bwanji chiwawa, ndipo kodi zimenezi ziyenera kukhudza bwanji mmene timasankhira zosangalatsa? (Gen. 6:11, 12; Sal. 11:5)

  Kodi tingatsanzire bwanji Nowa pamene talandira malangizo kudzera ku gulu la Yehova? (Gen. 6:22; 1 Yoh. 5:3)

 • Ŵerengani Genesis 7:1-9.

  Kodi mfundo yakuti Yehova anaona munthu wopanda ungwiroyo Nowa monga munthu wolungama imatilimbikitsa bwanji masiku ano? (Gen. 7:1; Miy. 10:16; Yes. 26:7)