Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 8: Zimphona pa Dziko

Nkhani 8: Zimphona pa Dziko

NGATI wina wake analinkudza kwa inu ndipo anali wamtali mapazi 9, mofanana ndi kufika pa siling’i ya nyumba yanu, kodi mukanaganizanji? Munthu’yo akakhala chimphona! Pa nthawi ina panali’di zimphona pa dziko. Baibulo limasonyeza kuti atate ao anali angelo ochokera kumwamba. Kodi zikanatero motani?

Dzianthu dzamphamvu dzandewu

Kumbukirani, mngelo woipa’yo Satana anali wotanganidwa kupanga bvuto. Anali kuyesa’di kuipitsa ngakhale angelo a Mulungu. M’kupita kwa nthawi, angelo ena anayamba kumumvetsera. Iwo analeka ntchito imene Mulungu anawapatsa kumwamba. Ndipo anadza pa dziko nadzipangira matupi aumunthu. Kodi mukudziwa chifukwa chake?

Baibulo limati chifukwa chakuti ana a Mulungu’wa anaona akazi okongola pa dziko nafuna kukhala nawo. Chotero anadza ku dziko nakwatira akazi’wa. Baibulo limati zimene’zi n’zolakwa, chifukwa chakuti Mulungu anapanga angelo kuti adzikhala kumwamba.

Angelo’wo ndi akazi ao atabala ana, ana’wa anali osiyana. Poyamba iwo sanaonekere kukhala osiyana kwambiri. Koma iwo anakula-kulabe, nakhala ndi mphamvu moonjezereka-onjezereka, kufikira anakhala zimphona.

Zimphona’zi zinali zoipa. Ndipo chifukwa cha kukula kwao kwambiri ndi mphamvu, zinkabvulaza anthu. Iwo anaumiriza ali yense kukhala woipa ngati iwo.

Enoke anali atafa, koma panali munthu wina pa dziko tsopano amene anali wabwino. Dzina la munthu’yu linali Nowa. Nthawi zonse anachita zimene Mulungu anafuna kuti iye achite.

Tsiku lina Mulungu anauza Nowa kuti nthawi inakwana yakuti Iye aononge anthu onse oipa. Koma iye akapulumutsa Nowa, banja lake ndi zinyama. Tiyeni tione m’mene Mulungu anachitira zimene’zi.

Genesis 6:1-8; Yuda 6.Mafunso

  • Kodi chinachitika n’chiyani pamene angelo ena a Mulungu anamvera Satana?
  • N’chifukwa chiyani angelo ena anasiya ntchito yawo kumwamba n’kubwera padziko lapansi?
  • N’chifukwa chiyani angelowo analakwa pobwera padziko lapansi n’kudzipangira matupi aumunthu?
  • Kodi ana a angelowo anali osiyana ndi anthu ena motani?
  • Monga momwe mukuonera pa chithunzipa, kodi ana a angelowo anachita chiyani pamene anasanduka zimphona?
  • Enoke atafa, kodi ndi munthu wabwino uti amene anakhala padziko lapansi, ndipo n’chifukwa chiyani Mulungu anamukonda?

Mafunso ena