Mayankho a Mafunso 10 Omwe Achinyamata Amadzifunsa
Pezani malangizo othandiza kuti zinthu zikuyendereni bwino.
FUNSO LOYAMBA
Kodi Ndimayendera Mfundo Ziti?
Kudziwa mfundo zimene mumayendera, zimene mumachita bwino, zimene mumalakwitsa komanso zolinga zanu kungakuthandizeni kuti muzisankha bwino zochita mukapanikizika.
FUNSO LACHIWIRI
Kodi Ndiyeneradi Kudandaula Ndi Mmene Ndimaonekera?
Kodi mumakhumudwa mukadziyang’anira pagalasi? Kodi ndi zinthu ziti zimene muyenera kusintha?
FUNSO LACHITATU
Kodi Ndingatani Kuti Ndizilankhulana Bwino ndi Makolo Anga?
Mfundo zimene zili m’nkhaniyi zingakuthandizeni kuti muzilankhulana bwino ndi makolo anu
FUNSO LA 4
Kodi Ndizitani Ndikalakwitsa Zinazake?
Tsiku lina mudzalakwitsa zinazake ndipo aliyense amalakwitsa ndithu. Koma kodi muyenera kutani zimenezi zikachitika?
FUNSO LA 5
Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa Kusukulu?
Pali zimene mungachite kuti anzanu asiye kukuvutitsani.
FUNSO LA 6
Ndingatani Kuti Ndisamangotengera Zochita za Anzanga?
Nthawi zina zingakhale zovuta kuti munthu alimbe mtima n’kuchita zolondola.
FUNSO LA 7
Kodi Ndingatani Ngati Wina Akundikakamiza Kuti Ndigone Naye?
Onani mavuto amene achinyamata amakumana nawo ngati achita chiwerewere.
FUNSO LA 8
Kodi Ndiyenera Kudziwa Chiyani Zokhudza Anthu Ogwiririra?
Nthawi zambiri achinyamata ndi amene amagwiriridwa. Kodi mungatani ngati izi zitakuchitikirani?
FUNSO LA 10
Kodi Baibulo Lingandithandize Bwanji?
Anthu ambiri amaganiza kuti Baibulo ndi buku la nthano, lachikale kapena lovuta kumvetsa. Koma zimenezi si zoona.