Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 4-A

Main Events of Jesus’ Earthly Life​—Leading Up to Jesus’ Ministry

Main Events of Jesus’ Earthly Life​—Leading Up to Jesus’ Ministry

Zochitika za M’mauthenga Abwino Anayi, Zondandalikidwa Motsatira Nthawi Imene Zinachitika

Matchati otsatirawa ali ndi mapu amene akusonyeza mmene Yesu anayendera komanso malo omwe analalikirako uthenga wabwino. Zizindikiro zangati mivi pamapu, sizikusonyeza njira zenizeni zimene anadutsa koma zikungosonyeza madera amene anafikako.

Zochitika Zotifikitsa pa Nthawi ya Utumiki wa Yesu

NTHAWI

MALO

CHOCHITIKA

MATEYU

MALIKO

LUKA

YOHANE

3 B.C.E.

Yerusalemu, m’kachisi

Mngelo Gabirieli akuuza Zekariya za kubadwa kwa Yohane M’batizi

   

1:5-25

 

Cha mu 2 B.C.E.

Nazareti; Yudeya

Mngelo Gabirieli akuuza Mariya za kubadwa kwa Yesu, Mariya achezera Elizabeti

   

1:26-56

 

2 B.C.E.

Dera la kumapiri la Yudeya

Kubadwa kwa Yohane M’batizi ndi kupatsidwa dzina; Zekariya anenera; Yohane azidzakhala m’chipululu

   

1:57-80

 

2 B.C.E., Cha pa Oct. 1

Betelehemu

Kubadwa kwa Yesu; ‘Mawu akhala munthu’

1:1-25

 

2:1-7

1:1-5, 9-14

Pafupi ndi Betelehemu; Betelehemu

Mngelo alengeza nkhani yabwino kwa abusa; angelo atamanda Mulungu; abusa apita kukaona mwana wakhandayo

   

2:8-20

 

Betelehemu; Yerusalemu

Yesu adulidwa (tsiku la 8); aperekedwa m’kachisi ndi makolo ake (tsiku la 40)

   

2:21-38

 

1 B.C.E. kapena 1 C.E.

Yerusalemu; Betelehemu; Iguputo; Nazareti

Okhulupirira nyenyezi apita kukaona Yesu; banja lithawira ku Iguputo; Herode apha ana aamuna; banja libwerera ku Iguputo ndi kukhazikika ku Nazareti

2:1-23

 

2:39, 40

 

12 C.E., Pasika

Yerusalemu

Yesu ali ndi zaka 12 ku kachisi akufunsa aphunzitsi

   

2:41-50

 
 

Nazareti

Abwerera ku Nazareti; apitiriza kumvera makolo ake; aphunzira ukalipentala; Mariya akhala ndi ana ena 4 aamuna, komanso ana aakazi (Mat. 13:55, 56; Maliko 6:3)

   

2:51, 52

 

29, chakumayambiriro kwa chaka

Chipululu, Mtsinje wa Yorodano

Yohane M’batizi ayamba utumiki wake

3:1-12

1:1-8

3:1-18

1:6-8, 15-28