Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Kuwala Kukuwonjezerekabe

Kuwala Kukuwonjezerekabe

AKHRISTU oona amadalira kwambiri Yehova chifukwa amadziwa kuti ndi amene amawathandiza kuti azimvetsa mfundo za m’Baibulo. Choncho, nthawi zonse amapemphera kwa Mulungu kuti ‘kuwala ndi choonadi chake’ ziziwatsogolera. (Sal. 43:3) Anthu ambiri m’dzikoli ali mumdima wandiweyani. Komabe, Yehova akuthandiza anthu ake kumvetsa mfundo zina zatsopano. Kumvetsa bwino mfundo zolondola kuli “ngati kuwala kwamphamvu kumene kumamka kuwonjezereka.” (Miy. 4:18) Yehova akuthandiza atumiki ake kuti aone kuwala kwakukulu posintha zinthu zina m’gulu lake, posintha mmene ankamvera mfundo zina komanso powathandiza kusintha makhalidwe awo. Ndiye kodi ndi mfundo ziti zomwe zafotokozedwanso mwatsopano zaka zapitazi?