Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

“Timakonda Kwambiri TV ya JW Broadcasting”

“Timakonda Kwambiri TV ya JW Broadcasting”

PA 6 OCTOBER, 2014, abale anaulutsa pulogalamu yoyamba yachingelezi pa TV yathu ya JW Broadcasting. * Kuyambira mwezi wa August 2015, mapulogalamu a pa TV imeneyi anayamba kumasuliridwa m’zinenero zoposa 70 n’cholinga choti abale ndi alongo a zinenero zinanso azipindula. Zikuoneka kuti abale ndi alongo padziko lonse akusangalala kwambiri ndi TV imeneyi. Koma kodi abale anachita zotani kuti TV imeneyi iyambe kugwira ntchito?

Choyamba, abalewa ankafunika kupeza malo oti kukhale situdiyo. Malowa anapezeka ku likulu lathu ku Brooklyn, m’nyumba yomwe imadziwika ndi dzina lakuti,  30 Columbia Heights. Pamene mlungu unkatha, zinthu zomwe zinali pamalowa zinali zitachotsedwa ndipo abale a m’dipatimenti yokonza zinthu anayamba kukonza malowa. Kenako abale okonza mapulani anajambula pulani ya situdiyo yooneka bwino komanso yokongola kwambiri. Abale ndi alongo ochokera m’madera osiyanasiyana m’dziko la United States anagwira ntchito mwakhama kwambiri pojambula pulaniyi komanso kukonza mmene angagwirire ntchitoyi mofulumira. Kafukufuku yemwe amayenera kuchitika kwa miyezi yambiri, anachitika m’masiku ochepa. Kenako dipatimenti yogula zinthu inayamba kuitanitsa katundu womangira situdiyoyi.

A dipatimenti yokonza zinthu anayambapo ntchito yokonza malowa ndipo atamaliza anayesa zipangizo zina zamagetsi kuti aone ngati zikugwira bwino ntchito. Pa nthawiyi, abale ndi alongo ochokera m’mayiko osiyanasiyana omwe amakonza nyimbo zathu, anali ali ku Patterson ndipo ankajambula nyimbo. Abalewa anapemphedwa kuti akonze ndiponso kujambula nyimbo yoti izidzaikidwa kumayambiriro ndi kumapeto kwa pulogalamuyi. Kagulu ka abale ena kanayamba kulemba mawu a vidiyo ndiponso kuyeserera. Abale a m’dipatimenti yojambula mavidiyo ku Brooklyn, ku Patterson, ku Wallkill ndiponso m’mayiko ena, anayambanso kujambula mavidiyo. Pamene abale a m’dipatimenti yokonza zinthu ankamaliza kukonza situdiyo n’kuti abale ena atayamba kale kukonzekera mavidiyo a miyezi ingapo yakutsogolo.

Situdiyo ya JW Broadcasting yomwe ili ku Brooklyn, ku New York

Tinafunsa munthu wina yemwe amadziwa bwino zokonza masitudiyo kuti atiuze kuti ntchitoyi imatenga nthawi yaitali bwanji. Iye ananena kuti ntchitoyi imatenga chaka ndi hafu kuti ithe. Koma abale ndi alongo athu anagwira ntchitoyi kwa miyezi iwiri yokha basi.

Zimene abale ndi alongowa anachita pogwira ntchitoyi zathandiza kwambiri. Pulogalamu ya mwezi ndi mwezi  imeneyi imaikidwa pa TV yathuyi Lolemba loyamba, mwezi uliwonse. Ndipo mwezi ukamatha, anthu amakhala ataonera pulogalamuyi maulendo oposa 2 miliyoni. Tikawerengetsera mavidiyo onse amene aulutsidwa, anthu amakhala ataonera mavidiyo a pa TV yathuyi maulendo oposa 10 miliyoni, mwezi ukamatha.

Munthu wina wa ku Kenya anati: “Pulogalamuyi yandithandiza kuti ndizikonda gulu la Yehova komanso abale a m’Bungwe Lolamulira. Ndikusangalala chifukwa ndili m’gulu lomwe anthu ake amakondana kuchokera pansi pa mtima.”

Koma kodi anthu akusangalaladi ndi TV imeneyi? Tiyeni tione zina zimene abale ndi alongo athu ananena.

  • Bambo wina wa ku Indonesia anati: “Lero ndasangalala kwambiri. Ine ndi mkazi wanga tangomaliza kumene kuonera pulogalamu ya mwezi wa May 2015. Pulogalamuyi ndi mphatso yamtengo wapatali kwambiri yochokera kwa Yehova. Tikuthokoza abale a m’Bungwe Lolamulira komanso abale ndi alongo onse omwe akuchita khama potikonzera mapulogalamu amenewa.”

  • M’bale wina wa ku Kenya anati: “M’mbuyomu zinali zovuta kuona abale a m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani. Koma imeneyi ndi mbiri yakale, chifukwa panopa tikutha kuwamva komanso kuwaona akukamba nkhani papulogalamuyi. Zimenezi zikuthandiza kuti abalewa tiwadziwe bwino komanso zikutithandiza kuona kuti tilidi m’gulu limodzi lapadziko lonse lapansi.”

  • Mlongo wina wa ku Britain ananena kuti: “Mwamuna wanga si wa Mboni, choncho zimavuta kuti ndizichita kulambira  kwa pabanja pamodzi ndi ana anga awiri. Kunena zoona, mapulogalamu amenewa andithandiza kwambiri. Amandithandiza kuona kuti sindili ndekha komanso amandilimbikitsa pamodzi ndi ana anga. Yehova watidalitsa kwambiri potipatsa mapulogalamu amenewa.”

  • Banja lina la ku Czech Republic linati: “Timakonda kwambiri TV ya JW Broadcasting moti tinasangalala kwabasi pulogalamuyi itayamba kuulutsidwa m’chinenero chathu. Timalimbikitsidwa tikamaona abale akutumikira Yehova mosangalala. Kungoyambira nthawi imene pulogalamuyi inayamba kuulutsidwa, timaona kuti ndifedi mbali ya gulu la Yehova, lomwe ndi lodabwitsa kwambiri.”

  • Munthu wina wa ku Brazil anati: “Ndikamvetsera nkhani za abale a m’Bungwe Lolamulira m’chinenero changa, ndimasangalala kwambiri. Ndimaona kuti mapulogalamuwa amandithandiza kukonda kwambiri Yehova.”

  • Munthu winanso wa ku Brazil anafotokoza mmene anamvera atangomaliza kumene kuonera pulogalamuyi. Iye anati: “Ndasangalala kwambiri ngati mmene ndinasangalalira pa nthawi imene ndinkabatizidwa, zaka 16 zapitazo. Zikomo kwambiri abale inu chifukwa cha TV imeneyi.”

Tikukhulupirira kuti Yehova apitirizabe kuthandiza abale ndi alongo athu kudzera pa TV imeneyi. TV imeneyi ithandiza kuti anthu azitamanda komanso kulemekeza Yehova.

^ ndime 1 TV ya JW Broadcasting ndi ya pa Intaneti ndipo mungaipeze pa adiresi iyi: tv.jw.org.