Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Bolivia: Abale akumanga ofesi ya omasulira m’chinenero cha Chiayimara ku El Alto

Zimene Zachitika M’chaka Chapitachi

Zimene Zachitika M’chaka Chapitachi

BAIBULO limasonyeza kuti Mulungu adzachita zinthu zosiyanasiyana pogwiritsa ntchito Ufumu wake. Ndipo lemba la Yesaya 9:7 limati, “Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.” Nayenso Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu ya Ufumuwu, anagwira ntchito modzipereka kwambiri pamene ankachita utumiki wake padziko lapansi. (Yoh. 2:17) Malipoti ali m’munsiwa akusonyeza kuti nawonso a Mboni za Yehova padziko lonse akutengera chitsanzo cha Yehova komanso Yesu. Iwo akuthandiza anthu kuona chikondi chimene Atate wathu Yehova, amatisonyeza.

El salvador: Msonkhano wachigawo wa 2015

M'CHIGAWO ICHI

“Timakonda Kwambiri TV ya JW Broadcasting”

Kodi abale anachita zotani kuti akonze situdiyoyi?

Pakufunika Kumanga Nyumba za Ufumu Mofulumira

Gulu lasintha zinthu zina pa nkhani ya zomangamanga kuti zithandize anthu ambiri kumanga Nyumba za Ufumu.

Kodi Ntchito Yomanga Ikuyenda Bwanji ku Warwick?

Dziwani mwachidule mmene ntchito yathu yomanga ikuyendera ku likulu la Mboni za Yehova.

Njira Imene Ikuthandiza Kulalikira Anthu Omwe Sapezeka Pakhomo

N’chiyani chinachititsa bambo Terry kukhulupirira kuti zimene anamva kwa Mboni za Yehova, linali yankho la pemphero lake?

Kuwala Kukuwonjezerekabe

M’chigawo chino, muona mmene Yehova akuthandizira anthu amene amamulambira.

Mwambo Wotsegulira Maofesi a Nthambi

Kumayambiriro kwa chaka cha 2015 a Mboni za Yehova ku Madagascar ndi ku Indonesia anachita mwambo wotsegulira maofesi a nthambi m’mayiko awo.

Baibulo la Dziko Lapansi Latsopano Lamasuliridwa M’zinenero Zinanso Zambiri

M’chaka cha utumiki cha 2015, Mabaibulo a m’zinenero zokwana 16 anatulutsidwa.

Lipoti la Milandu

Padziko lonse, a Mboni za Yehova akupitirizabe kutsutsidwa ndi akuluakulu a boma komanso zipembedzo zina.

Malipoti Apadera—Zochitika M’mayiko Osiyanasiyana

Ndalama zimene Ken ankaponya m’kabokosi kake zinathandiza pa nthawi yomanga Nyumba ya Ufumu.