Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mwambo wa Chikumbutso—Lachisanu pa 3 April, 2015

Mwambo wa Chikumbutso—Lachisanu pa 3 April, 2015

MIPINGO inayamba kugawira timapepala toitanira anthu kumwambo wokumbukira imfa ya Yesu Khristu komanso kuti adzamvetsere nkhani yosonyeza mmene imfa imeneyi imatithandizira. Ntchitoyi inayamba Loweruka pa 7 March, 2015 ndipo inatenga milungu 4. Abale ndi alongo anaitanira anthu ambiri kumwambowu powapatsa timapepala, powaimbira foni komanso powalembera kalata. Kodi ntchito imene abale ndi alongo anagwirayi inathandizadi? Inde inathandiza kwambiri. Tikutero chifukwa pa tsiku la mwambo wapaderawu, Lachisanu pa 3 April, panabwera anthu okwana 19,862,783. Panopo abale ndi alongo akuyesetsa kuthandiza anthu achidwi amene anabwera pamwambowu kuti apitirizebe kusonkhana nafe. Zimenezi zingawathandize kuti azilambira Mulungu woona komanso kuti akhale naye pa ubwenzi, n’kudzalandira madalitso amene watikonzera m’tsogolomu.—Mika 4:2.