Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 INDONESIA

Njira Zimene Poyamba Ankagwiritsa Ntchito Polalikira

Njira Zimene Poyamba Ankagwiritsa Ntchito Polalikira

Kulalikira pa Wailesi

MU 1933, abale anakonza zoti nkhani zojambulidwa zimene M’bale Rutherford ankakamba m’Chingelezi ziziulutsidwa pa wailesi ina ya m’dziko la Indonesia. Komanso munthu wina amene ankaphunzira Baibulo ankamasulira nkhani zina za M’bale Rutherford m’Chidatchi n’kuziulutsa pa wailesiyi. Zimenezi zinachititsa kuti anthu ambiri ayambe kuphunzira Baibulo. Zinathandizanso kuti abale agawire mabuku ambiri.

Wailesiyi inaulutsa nkhani yomwe M’bale Rutherford anakamba mosapita m’mbali ya mutu wakuti, “Chiyambukiro cha Chaka Chopatulika pa Mtendere.” Atsogoleri achipembedzo cha Katolika atamva zimene zinakambidwa m’nkhaniyi, anakwiya kwambiri. * Choncho anatumiza anthu kuti akagwire M’bale De Schumaker, yemwe anabweretsa nkhanizi kuti ziulutsidwe pa wailesi. Atsogoleriwa anamuimba mlandu wonena zinthu zabodza, wonyoza chipembedzo komanso woyambitsa chidani. M’baleyu ananena mfundo zamphamvu m’khoti podziteteza, komabe anamulipiritsa ndalama zokwana magiuda 25 * komanso ndalama zina zomwe khoti linagwiritsa ntchito poyendetsa mlanduwo. Nyuzipepala zitatu  zinalemba mmene nkhaniyi inayendera. Zimenezi zinathandiza kuti anthu adziwe za Mboni za Yehova.

Kulalikira pa Sitima Yapamadzi

Pa July 15, 1935, sitima yapamadzi ya Mboni za Yehova yotchedwa Lightbearer inafika ku Jakarta. Sitimayi, yomwe inali yaitali mamita 16, inali itayenda ulendo wapanyanja kwa miyezi 6 kuchokera  ku Sydney, m’dziko la Australia. M’sitimayi munali apainiya 7 omwe ankafunitsitsa kukalalikira uthenga wabwino m’mayiko a Indonesia, Singapore ndi Malaysia.

Kwa zaka zoposa ziwiri, apainiyawa anafika kumadoko ang’onoang’ono komanso akuluakulu a m’dziko lonse la Indonesia ndipo anagawira mabuku ambiri ofotokoza Baibulo. Mlongo Jean Deschamp ananena kuti sitima ikamayandikira doko lililonse laling’ono, “abale ankatsegula makina omwe tinkagwiritsa ntchito poulutsa nkhani za M’bale J. F. Rutherford, yemwe pa nthawiyo anali pulezidenti wa Watch Tower Society. Anthu omwe ankakhala kumidzi ya ku Malay ankadabwa kwambiri kuona chisitima chikufika komanso mawu akumveka m’mwamba chifukwa zoterezi anali asanazionepo.”

Atsogoleri achipembedzo anakwiya kwambiri chifukwa cha abale omwe ankalalikira molimba mtimawa. Choncho anakakamiza akuluakulu a boma kuti aletse sitima ija kufika pamadoko a ku Indonesia. Kenako mu December 1937, abalewo anabwerera ku Australia atagwira ntchito yotamandika.

Abale omwe ankalalikira pa sitima ya Lightbearer

^ ndime 2 Nkhani zimene M’bale Rutherford ankakamba zinkanena mosapita m’mbali zinthu zachinyengo zimene atsogoleri achipembedzo cha Katolika ankachita pa nkhani zandale, zamalonda komanso zokhudza kupemphera.

^ ndime 2 Ndalamazi ndi zokwana madola 300 a ku America.