Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 INDONESIA

Tinasangalala Titadziwa Kuti Ndife Pachibale

Yofotokozedwa ndi Linda Komanso Sally Ong

Tinasangalala Titadziwa Kuti Ndife Pachibale

Linda: Ndili ndi zaka 12, mayi anga anandiuza kuti ndili ndi mng’ono wanga amene sindinamuonepo yemwe akuleredwa ndi banja lina. Atandiuza zimenezi, ndinayamba kuganiza kuti mwina nayenso ali ndi vuto losamva ngati ineyo.

Sally: Sindinkadziwa kuti amene ankandilera sanali makolo anga enieni. Mayi anga ongondilerawo ankandimenya kwambiri komanso ankanditenga ngati wantchito. Popeza ndili ndi vuto losamva, zinkangowonjezera mavuto anga moti sindinkasangalala. Kenako ndinakumana ndi a Mboni za Yehova ndipo ndinayamba kuphunzira Baibulo. Mayi angawa atadziwa zimenezi, anandikwapula koopsa ndi lamba ndipo anasintha maloko a nyumba yathu n’kunditsekera kuti ndisamatuluke. Ndili ndi zaka 20, ndinathawa pakhomo ndipo a Mboni ananditenga n’kumandisunga. Ndinapitirizabe kuphunzira Baibulo ndipo mu 2012 ndinabatizidwa.

 Linda: Ndili ndi zaka 20, ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Kenako ndinayamba kupita kumisonkhano ya Mboni yomwe inkachitikira ku Jakarta, chifukwa ankamasulira nkhani zake m’chinenero chamanja. Kumeneku ndinakumana ndi anthu ambiri omwe anali ndi vuto lofanana ndi langa. Ndinakumananso ndi Sally, yemwe anali wa Mboni ndipo ankakhala ku North Sumatra. Nditakumana naye, zinkangokhala ngati tinakumanapo kale, koma sindinkaganiza zoti angakhale m’bale wanga.

Sally: Ndinayamba kugwirizana kwambiri ndi Linda. Ndinkaona kuti timafanana, koma nanenso sindinkaganiza zoti ndi m’bale wanga.

Linda: Mu August 2012, kutatsala tsiku limodzi kuti ndibatizidwe, ndinayamba kufunitsitsa nditakumana ndi mng’ono wanga amene mayi anga anandiuza kuti ankaleredwa ndi banja lina. Ndinapemphera kwa Yehova n’kumuuza kuti: “Ndithandizeni kupeza m’bale wanga chifukwa ndikufuna kuti nayenso akudziweni.” Pasanapite nthawi, mayi anga analandira meseji kuchokera kwa munthu wina yemwe ankadziwa mng’ono wangayu. Kungochokera nthawi imeneyo, ndinayamba kufufuza kumene Sally ankakhala.

Sally: Linda atandiuza kuti ndi m’bale wanga, nthawi yomweyo ndinanyamuka kupita ku Jakarta kuti ndikakumane naye. Pa ulendowu ndinakwera ndege ndipo nditangofika, ndinaona Linda, bambo, mayi komanso mkulu wanga wina akundidikirira. Zimenezi zinandikhudza kwambiri moti tinakumbatirana ndipo mayi anga ndi amene anandikumbatira kwa nthawi yaitali. Aliyense ankangolira ndipo bambo komanso mayi anga anandipepesa kwambiri chifukwa chondipereka kwa makolo ena kuti akandilere. Kenako tinakumbatirananso ndipo tinalira kwambiri.

Linda: Popeza tinakulira kosiyana, tinayamba kuphunzirana kuti tizigwirizana ndipo timakondana kwambiri.

Sally: Panopa ndimakhala limodzi ndi Linda komanso timasonkhana mumpingo umodzi wachinenero chamanja ku Jakarta.

Linda: Ine ndi Sally sitinkadziwana kwa zaka 20. Timathokoza kwambiri Yehova kuti anatithandiza kuti tikumane patapita zaka zambiri.