Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 INDONESIA

Mfundo Zachidule Zokhudza Dziko la Indonesia

Mfundo Zachidule Zokhudza Dziko la Indonesia

Mmene Dzikoli Lilili Dziko la Indonesia ndi limene lili ndi zilumba zambiri padziko lonse lapansi. Zilumbazi ndi zoposa 17,500 ndipo zili m’dera la pakatim’pakati pa dziko lonse lapansi komwe kumatentha komanso kugwa mvula yambiri. Zina zili kumbali ya Australia ndipo zina zili kumbali ya kumayiko a ku Asia. M’zilumba zambiri muli mapiri komanso nkhalango zowirira. M’dzikoli muli mapiri oposa 100 omwe akhoza kuphulika nthawi ina iliyonse ndipo ndi dziko lomwe kumaphulika mapiri kawirikawiri kuposa kwina kulikonse.

Anthu Dziko la Indonesia ndi la nambala 4 pa mayiko amene ali ndi anthu ambiri padziko lonse lapansi. Mayiko atatu oyambirira ndi China, India ndi United States. M’dzikoli mumapezeka mitundu ya anthu yoposa 300. Anthu ambiri ndi Ajava komanso Asunda, moti pafupifupi hafu ya anthu okhala m’dzikoli ndi ochokera m’mitundu imeneyi.

 Chipembedzo Pafupifupi anthu 9 pa anthu 10 alionse m’dzikoli ndi Asilamu. Ena ali m’chipembedzo cha Chihindu, Chibuda ndipo Akhristu alipo ochepa kwambiri. Anthu enanso ambiri m’dzikoli amatsatira miyambo yachipembedzo cha makolo awo.

Chiyankhulo Anthu okhala m’zilumba za dziko la Indonesia amayankhula ziyankhulo zoposa 700. Anthu amene amayankhula ziyankhulo zosiyana, amagwiritsa ntchito chinenero cha Chimalaya akafuna kuti amvane.

Ntchito Zawo Anthu ambiri ndi alimi koma ena amachita bizinezi zosiyanasiyana. M’dzikoli muli miyala yambiri ya mtengo wapatali, mafuta, gasi, komanso amacheka matabwa ambiri. Dzikoli limagulitsa kumayiko ena labala wopangira matayala komanso mafuta opangidwa kuchokera kumitengo yakanjedza.

Chakudya Anthu ambiri amadya mpunga. Anthuwa amakonda kudya mpunga wa ndiwo zamasamba ndi mazira, nyama yowotcha komanso masamba osaphika opaka chiponde.

Nyengo Derali ndi lotentha komanso kumagwa mvula yambiri. Chifukwa cha mmene mphepo ya m’dzikoli imayendera, kumagwa mvula yamphepo komanso kumachita mabingu koma nthawi zina kumakhala kouma.