Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 INDONESIA

Tinapulumuka Chifukwa Chotsatira Malangizo

Blasius da Gomes

Tinapulumuka Chifukwa Chotsatira Malangizo
  • CHAKA CHOBADWA 1963

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1995

  • MBIRI YAKE Mkulu amene anasamalira nkhosa mwachikondi, pa nthawi imene panali mavuto a zachipembedzo mumzinda wa Ambon, womwe ndi mbali ya zilumba za Maluku.

PA 19 January 1999, Asilamu ndi Akhristu anayamba kumenyana koopsa chifukwa ankadana kwambiri. Maguluwa ankamenyana pa mtunda wa makilomita atatu kuchokera kumene ndinkakhala. *

Nditatsimikizira kuti banja langa ndi lotetezeka, ndinaimbira foni ofalitsa ena kuti ndidziwe mmene alili. Ndinawalimbikitsa kuti asachite mantha komanso kuti ayesetse kupewa kupita kumalo amene kunkachitika zachipolowezi. Kenako akulu anakalimbikitsa abale ndi alongo powauza mfundo za m’Malemba komanso anawalimbikitsa kuti azisonkhana m’timagulu.

A ku ofesi ya nthambi anatilimbikitsa kuti tiuze abale ndi alongo amene ankakhala m’madera omwe anthu ankamenyana kwambiri, kuti asamukeko. Tinauza mabanja angapo malangizo amenewa, koma m’bale wina amene sanamvere anaphedwa ndi gulu la anthu olusa. Aliyense amene anamvera malangizo ochokera ku ofesi ya nthambi anapulumuka.

^ ndime 1 Kumenyanaku kunkachitika m’madera onse a ku Maluku ndipo kunatenga pafupifupi zaka ziwiri. Zipolowezi zinachititsa kuti anthu ambiri athawe m’nyumba zawo.