Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 INDONESIA

Mpainiya Wopanda Mantha

André Elias

Mpainiya Wopanda Mantha
  • CHAKA CHOBADWA 1915

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1940

  • MBIRI YAKE Mpainiya amene anakhalabe wolimba mtima pa nthawi imene ankafunsidwa mafunso komanso kuwopsezedwa ndi apolisi.

PA NTHAWI ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, M’bale Elias limodzi ndi mkazi wake Josephine, anakaonekera pamaso pa akuluakulu a boma mumzinda wa Sukabumi ku West Java. Gulu la apolisi a ku Japan lotchedwa Kempeitai lomwe linali loopsa kwambiri ndi limene linawaitana kuti likawafunse mafunso. Apolosiwa anayamba kuphaphalitsa M’bale Elias ndi mafunso komanso kumuwopseza. Anamufunsa mafunso monga akuti, ‘Kodi a Mboni za Yehova ndi ndani?’ ‘Kodi n’zoona kuti mumalimbana ndi boma la Japan?’ komanso lakuti, ‘Kodi ndiwe kazitape?’

M’bale Elias anawayankha kuti, “Ndife atumiki a Mulungu Wamphamvuyonse ndipo sitinalakwe chilichonse.” Atanena zimenezi, mkulu wa apolisiyo anatenga chimpeni chomwe chinali pakhoma n’kuchinyamula m’mwamba.

Kenako mkuluyo ananena mwaukali kuti: “Inetu ndikhoza kukupha.” Atamva zimenezi, M’bale Elias anaweramira patebulo n’kuyamba kupemphera chamumtima. Anthu onse anangokhala chete ndipo patadutsa kanthawi, mkulu wa apolisi uja anaseka n’kunena kuti: “Ndiwe munthu wolimba mtima.”  Kenako anaitananso Mlongo Elias kuti amufunse mafunso ndipo zomwe anayankha zitagwirizana ndi zimene M’bale Elias ananena, wapolisiyo anati: “Basi zipitani, ndadziwa kuti siinu akazitape.”

Patatha miyezi ingapo, ‘abale achinyengo’ ananena zinthu zabodza kwa akuluakulu a boma zokhudza M’bale Elias. Zimenezi zinachititsa kuti m’baleyu amangidwe. (2 Akor. 11:26) M’bale Elias anaikidwa m’ndende ina ndipo oyang’anira ndendeyo sankamupatsa chakudya. Ndiye kuti asafe ndi njala, m’baleyu ankachita kutoleza zakudya m’ngalande. Koma iye anakhalabe wokhulupirika. Tsiku lina mkazi wake atabwera kudzamuona kundendeko, M’bale Elias anamunong’oneza kuti: “Usade nkhawa. Kaya andipha kapena ayi, sindisiya kukhala wokhulupirika kwa Yehova. Ndilolera kuti andiphe kusiyana n’kuti ndichite zinthu mosakhulupirika.”

Atakhala m’ndende kwa miyezi 6, m’baleyu anakaonekera kukhoti lalikulu la ku Jakarta komwe anakawina mlandu wake ndipo anamasulidwa.

Patadutsa zaka 30, boma la Indonesia linaletsanso ntchito ya Mboni za Yehova. Zitatero, mkulu woona za malamulo mumzinda wa Manado ku North Sulawesi, anaitanitsanso M’bale Elias kuti akamufunse mafunso. Anamufunsa kuti: “Kodi ukudziwa kuti a Mboni za Yehova ndi oletsedwa m’dziko lino?”

M’baleyu anamuyankha kuti, “Ee, ndikudziwa.”

Kenako anamufunsanso kuti: “Ndiye kodi panopa wakonzeka kusiya chipembedzo chakochi?”

M’bale Elias anaweramira kutsogolo n’kudziguguda pachifuwa kenako analankhula mwamphamvu kuti: “Mukhoza kundipha, koma simungandisiyitse chipembedzo changa.”

Atayankhula mawu amenewa, mkuluyo anamuuza kuti azipita ndipo sanamuvutitsenso.

M’bale André Elias anamwalira m’chaka cha 2000 ali ndi zaka 85 ndipo anali atachita upainiya kwa zaka pafupifupi 60.