Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 INDONESIA

Kunayambika Kagulu Kenakake ka Chipembedzo

Kunayambika Kagulu Kenakake ka Chipembedzo

CHAKUMAPETO kwa zaka za m’ma 1930, kudera lozungulira nyanja ya Toba, yomwe ili ku North Sumatra, kunayambika kagulu kenakake kachipembedzo. Kaguluka kankatchedwa Bibelkring, dzina lachidatchi lomwe limatanthauza gulu la ophunzira Baibulo. Kaguluka kanayamba mu 1936 aphunzitsi ena atalandira mabuku kwa mpainiya wina, yemwe n’kutheka kuti anali Eric Ewins. Tikutero chifukwa mpainiyayu ndi amene analalikira m’dera lozungulira nyanja ya Toba. Zimene anthuwa anawerenga zinawachititsa kuti atuluke m’tchalitchi cha Bataki ndipo anakhazikitsa timagulu ta ophunzira Baibulo. Anthu amene ankasonkhana m’timaguluti anachuluka ndipo anayamba kupezeka m’madera ambiri. *

Mlongo Dam Simbolon yemwe kale anali m’kagulu ka Bibelkring

Anthu a m’kaguluka anadziwa mfundo zambiri zolondola za m’Baibulo chifukwa cha mabuku amene apainiya anawasiyira. Munthu wina yemwe poyamba anali m’kaguluka, dzina lake Dame Simbolon, anayamba kuphunzira choonadi mu 1972. Iye anati: “Anthuwo ankakana kuchitira sailuti mbendera, kuchita Khirisimasi komanso kukondwerera masiku obadwa. Ena ankalalikiranso kunyumba ndi nyumba.” Koma chifukwa choti sankathandizidwa ndi gulu la Mulungu, anthuwa anayamba kuyendera maganizo awo. Mlongo wina, dzina lake Limeria Nadap-Dap, yemwe poyamba analinso m’kagulu kameneka, ananena kuti: “Akazi sankaloledwa kuphoda, kuvala ndolo kapena zibangili, kuvala zovala zamakono ngakhalenso nsapato. Anthuwa ankakananso kukhala ndi chiphaso chosonyeza kuti ndi nzika za dziko la Indonesia. Zimenezi zinakwiyitsa kwambiri akuluakulu a boma.”

Patapita nthawi, kaguluka kanagawanika ndipo kanatha. Kenako apainiya atapitanso m’dera la kunyanja ya Toba, anthu ambiri omwe poyamba anali m’kaguluka anaphunzira choonadi.

^ ndime 1 Anthu ena amanena kuti anthu omwe ankasonkhana m’timaguluti analipo masauzande ambiri.