Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

N’chifukwa Chiyani Mumaona Kuti Kulambira Koyera N’kofunika?

N’chifukwa Chiyani Mumaona Kuti Kulambira Koyera N’kofunika?

Masomphenya a Ezekieli okhudza kachisi analimbikitsa Ayuda amene anali ku ukapolo chifukwa anawapatsa chiyembekezo choti kulambira koyera kudzabwezeretsedwa. Masiku otsiriza ano, kulambira koyera ‘kwakhazikika pamwamba pa nsonga za mapiri,’ ndipo ifeyo tili m’gulu la anthu a mitundu yonse omwe akhamukira kumeneko. (Yes. 2:2) Kodi mumasonyeza kuyamikira mwayi umene muli nawo wodziwa komanso kutumikira Yehova?

MADALITSO AMENE TIMAPEZA:

  • Timalandira chakudya chauzimu chochuluka chomwe chimatithandiza kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri, malangizo otithandiza pa moyo komanso tikuyembekezera zinthu zabwino mtsogolo.​—Yes. 48:17, 18; 65:13; Aroma 15:4

  • Timasangalala ndi ubale wapadziko lonse.​—Sal. 133:1; Yoh. 13:35

  • Tili ndi mwayi wokhala antchito anzake a Mulungu pogwira nawo ntchito yolalikira imene sidzachitikanso.​—Mac. 20:35; 1 Akor. 3:9

  • Timakhala ndi “mtendere wa Mulungu” umene umatilimbikitsa pa nthawi ya mavuto.​—Afil. 4:6, 7

  • Timakhala ndi chikumbumtima choyera.​—2 Tim. 1:3

  • Timakhala pa “ubwenzi wolimba ndi Yehova.”​—Sal. 25:14

Kodi ndingasonyeze m’njira ziti kuti ndimaona kuti kulambira koyera n’kofunika?